< Masalimo 143 >

1 Salimo la Davide. Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza. 2 Musazenge mlandu mtumiki wanu, pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu. 3 Mdani akundithamangitsa, iye wandipondereza pansi; wachititsa kuti ndikhale mu mdima ngati munthu amene anafa kale. 4 Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga; mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa. 5 Ndimakumbukira masiku amakedzana; ndimalingalira za ntchito yanu yonse, ndimaganizira zimene manja anu anachita. 6 Ndatambalitsa manja anga kwa Inu; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma. (Sela) 7 Yehova ndiyankheni msanga; mzimu wanga ukufowoka. Musandibisire nkhope yanu, mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje. 8 Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika, pakuti ine ndimadalira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo, pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga. 9 Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova, pakuti ndimabisala mwa Inu. 10 Phunzitseni kuchita chifuniro chanu, popeza ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala. 11 Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga. 12 Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga; wonongani adani anga, pakuti ndine mtumiki wanu.

< Masalimo 143 >