< Masalimo 136 >

1 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. 2 Yamikani Mulungu wa milungu. 3 Yamikani Ambuye wa ambuye, 4 Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu, 5 Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba, 6 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi, 7 Amene anapanga miyuni ikuluikulu, 8 Dzuwa lilamulire usana, 9 Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku, 10 Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto, 11 Natulutsa Israeli pakati pawo, 12 Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka, 13 Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati, 14 Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo, 15 Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira, 16 Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu 17 Amene anakantha mafumu akuluakulu, 18 Napha mafumu amphamvu, 19 Siloni mfumu ya Aamori, 20 Ogi mfumu ya Basani, 21 Napereka dziko lawo ngati cholowa, 22 Cholowa cha mtumiki wake Israeli; 23 Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa, 24 Amene anatimasula kwa adani athu, 25 Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse, 26 Yamikani Mulungu wakumwamba,

< Masalimo 136 >