< Masalimo 134 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova, amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova. 2 Kwezani manja anu mʼmalo opatulika ndipo mutamande Yehova. 3 Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.

< Masalimo 134 >