< Masalimo 124 >

1 Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli, 2 akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo, 3 iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo; 4 chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola, 5 madzi a mkokomo akanatikokolola. 6 Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. 7 Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. 8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

< Masalimo 124 >