< Masalimo 121 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? 2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. 3 Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera. 4 Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona. 5 Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja. 6 Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku. 7 Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. 8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.

< Masalimo 121 >