< Masalimo 12 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide. Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu.
To the chief Musician. Upon Sheminith. A Psalm of David. Save, Jehovah, for the godly man is gone; for the faithful have failed from among the children of men.
2 Aliyense amanamiza mʼbale wake; ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.
They speak falsehood every one with his neighbour: [with] flattering lip, with a double heart, do they speak.
3 Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo ndi pakamwa paliponse podzikuza.
Jehovah will cut off all flattering lips, the tongue that speaketh proud things,
4 Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu; pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”
Who have said, With our tongue will we prevail, our lips are our own: who [is] lord over us?
5 “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.”
Because of the oppression of the afflicted, because of the sighing of the needy, now will I arise, saith Jehovah, I will set [him] in safety, at whom they puff.
6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri.
The words of Jehovah are pure words, silver tried in the furnace of earth, purified seven times.
7 Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.
Thou, Jehovah, wilt keep them, thou wilt preserve them from this generation for ever.
8 Oyipa amangoyendayenda ponseponse anthu akamayamikira zochita zawo.
The wicked walk about on every side, when vileness is exalted among the children of men.

< Masalimo 12 >