< Masalimo 114 >

1 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo, 2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake. 3 Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo; 4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa. 5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa? iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo? 6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna, inu timapiri, ngati ana ankhosa? 7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi, pamaso pa Mulungu wa Yakobo, 8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime, thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.

< Masalimo 114 >