< Masalimo 112 >

1 Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake. 2 Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa. 3 Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha. 4 Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima. 5 Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo. 6 Ndithu sadzagwedezeka; munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya. 7 Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova. 8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano. 9 Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu. 10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.

< Masalimo 112 >