< Masalimo 100 >

1 Salimo. Nyimbo yothokoza. Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi. 2 Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero. 3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake. 4 Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake. 5 Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

< Masalimo 100 >