< Miyambo 9 >

1 Nzeru inamanga nyumba yake; inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri. 2 Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake; inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake. 3 Nzeruyo inatuma adzakazi ake, kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti, 4 “Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!” Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti, 5 “Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza. 6 Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo; yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.” 7 Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo; aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake. 8 Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda. 9 Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru; ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake. 10 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu. 11 Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa. 12 Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa; ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha. 13 Uchitsiru ndi mkazi waphokoso, wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu. 14 Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake, pamalo aatali a mu mzinda, 15 kuti aziyitana anthu ongodutsa, amene akunka nayenda njira zawo. 16 Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati, 17 “Madzi akuba ndiye amatsekemera; chakudya chodya mobisa ndi chokoma!” 18 Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya. (Sheol h7585)

< Miyambo 9 >