< Mateyu 4 >

1 Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.
Then Jesus was led up by the Spirit into the wilderness to be tempted by the devil.
2 Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala.
And when he had fasted forty days and forty nights, he was hungry afterward.
3 Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”
And the tempter came and said to him, "If you are the Son of God, command that these stones become bread."
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’”
But he answered and said, "It is written, 'Humankind cannot live by bread alone, but by every word that proceeds out of the mouth of God.'"
5 Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu.
Then the devil took him into the holy city. He set him on the pinnacle of the temple,
6 Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa: “‘Adzalamulira angelo ake za iwe, ndipo adzakunyamula ndi manja awo kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’”
and said to him, "If you are the Son of God, throw yourself down, for it is written, 'He will put his angels in charge of you.' and, 'In their hands they will lift you up, so that you will not strike your foot against a stone.'"
7 Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’”
Jesus said to him, "Again, it is written, 'Do not test the Lord your God.'"
8 Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo.
Again, the devil took him to a very high mountain, and showed him all the kingdoms of the world, and their glory.
9 Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”
And he said to him, "I will give you all of these things, if you will fall down and worship me."
10 Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’”
Then Jesus said to him, "Go away, Satan. For it is written, 'You are to worship the Lord your God, and serve him only.'"
11 Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.
Then the devil left him, and look, angels came and served him.
12 Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya.
Now when he heard that John was delivered up, he withdrew into Galilee.
13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali;
And leaving Nazareth, he came and lived in Capernaum, which is by the sea, in the region of Zebulun and Naphtali,
14 pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
that it might be fulfilled which was spoken through Isaiah the prophet, saying,
15 “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani, Galileya wa anthu a mitundu ina,
"The land of Zebulun and the land of Naphtali, toward the sea, beyond the Jordan, Galilee of the nations.
16 anthu okhala mu mdima awona kuwala kwakukulu; ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa kuwunika kwawafikira.”
The people sitting in darkness have seen a great light, and those living in the land and shadow of death, on them a light has dawned."
17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
From that time on, Jesus began to preach and say, "Repent, for the kingdom of heaven is near."
18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi.
And walking by the sea of Galilee, he saw two brothers: Simon, who is called Peter, and Andrew, his brother, casting a net into the sea; for they were fishermen.
19 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
And he said to them, "Come, follow me, and I will make you fishers of people."
20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
And they immediately left their nets and followed him.
21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana.
Going on from there, he saw two other brothers, James the son of Zebedee, and John his brother, in the boat with Zebedee their father, mending their nets, and he called them.
22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.
And they immediately left the boat and their father, and followed him.
23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.
And Jesus went about in all Galilee, teaching in their synagogues, and preaching the Good News of the Kingdom, and healing every disease and every sickness among the people.
24 Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa.
And the report about him went out into all Syria, and they brought to him all who were sick, afflicted with various diseases and torments, possessed with demons, and epileptics, and paralytics; and he healed them.
25 Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.
And large crowds from Galilee, and Decapolis, and Jerusalem, and Judea, and from beyond the Jordan followed him.

< Mateyu 4 >