< Mateyu 24 >

1 Yesu anatuluka mʼNyumba ya Mulungu ndipo akuchoka ophunzira ake anadza kwa Iye ndi kumuonetsa mamangidwe a Nyumbayo.
Leaving the Temple Courts, Jesus was walking away, when his disciples came up to draw his attention to the Temple buildings.
2 Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuona zinthu zonsezi? Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti palibe mwala pano umene udzasiyidwe pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
‘Do you see all these things?’ was his answer. ‘I tell you, not a single stone will be left here on another, which will not be thrown down,’
3 Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, “Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?” (aiōn g165)
so, while Jesus was sitting on the Mount of Olives, his disciples came up to him privately and said, ‘Tell us when this will be, and what will be the sign of your coming, and of the close of the age.’ (aiōn g165)
4 Yesu anayankha kuti, “Onetsetsani kuti wina asakunyengeni.
Jesus replied to them, ‘See that no one leads you astray;
5 Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati, ‘Ndine Khristu,’ ndipo adzanyenga ambiri.
for, many will take my name, and come saying “I am the Christ,” and will lead many astray.
6 Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike.
You will hear of wars and rumours of wars; take care not to be alarmed, for such things must occur; but the end is not yet here.
7 Mtundu ndi mtundu udzawukirana, ndipo ufumu ndi ufumu udzawukirana. Kudzakhala njala ndi zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana.
For nation will rise against nation and kingdom against kingdom, and there will be famines and earthquakes in various places.
8 Zonsezi ndi chiyambi chabe cha zowawa.
All this, however, will be but the beginning of the birth pangs!
9 “Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine.
When that time comes, they will give you up to persecution, and will put you to death, and you will be hated by all nations because of me.
10 Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake,
And then many will fall away, and will betray one another, and hate one another.
11 ndipo aneneri onama ambiri adzaoneka ndi kunyenga anthu ambiri.
Many false prophets, also, will appear and lead many astray;
12 Chifukwa cha kuchuluka kwa zoyipa, chikondi cha ambiri chidzazirala,
and, owing to the increase of wickedness, the love of most will grow cold.
13 koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.
Yet the person who endures to the end will be saved.
14 Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”
This good news of the kingdom will be proclaimed throughout the world as a witness to all nations; and then will come the end.
15 “Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire.
As soon, then, as you see “the Foul Desecration,” mentioned by the prophet Daniel, standing in the Holy place,’ (the reader must consider what this means)
16 Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire ku mapiri.
‘then those of you who are in Judea must take refuge in the mountains;
17 Yemwe ali pa denga la nyumba yake asatsike kukatulutsa chinthu chilichonse mʼnyumba.
and a man on the housetop must not go down to get the things that are in his house;
18 Yemwe ali ku munda asapite kukatenga mkanjo wake.
nor must one who is on their farm turn back to get his cloak.
19 Kudzakhala koopsa kwambiri masiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi kwa oyamwitsa!
Alas for pregnant women, and for those who are nursing infants in those days!
20 Pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzachitike nthawi yozizira kapena pa Sabata.
Pray, too, that your flight may not take place in winter, nor on a Sabbath;
21 Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena.
for that will be a time of great distress, the like of which has not occurred from the beginning of the world down to the present time – no, nor ever will again.
22 Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.
Had not those days been limited, not a single soul would escape; but for the sake of God’s people a limit will be put to them.
23 Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire.
At that time, if anyone should say to you “Look! Here is the Christ!” or “Here he is!”, do not believe it;
24 Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero.
for false Christs and false prophets will arise, and will display great signs and marvels, so that, were it possible, even God’s people would be led astray.
25 Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
Remember, I have told you beforehand.
26 “Ndiye ngati wina akuwuzani inu kuti, ‘Uyo ali ku chipululu,’ inu musapiteko; kapena akati, ‘Uyu ali kuno mʼchipinda chamʼkati,’ musakhulupirire.
Therefore, if people say to you “He is in the wilderness!”, do not go out there; or “He is in an inner room!”, do not believe it;
27 Monga momwe mphenzi ingʼanima kuchokera kummawa kupita kumadzulo, momwemonso kudzakhala kubwera kwa Mwana wa Munthu.
for, just as lightning will start from the east and flash across to the west, so will it be with the coming of the Son of Man.
28 Kulikonse kuli chinthu cha kufa, makwangwala adzasonkhanako.
Wherever a dead body lies, there will the vultures flock.
29 “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, “‘dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzawala; nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
Immediately after the distress of those days, the sun will be darkened, the moon will not give her light, the stars will fall from the heavens, and the forces of the heavens will be convulsed.
30 “Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.
Then will appear the sign of the Son of Man in the heavens; and all the peoples of the earth will mourn, when they see the Son of Man coming on the clouds of the heavens, with power and great glory;
31 Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
and he will send his angels, with a great trumpet, and they will gather his people round him from the four winds, from one end of heaven to the other.
32 “Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira.
‘Learn the lesson taught by the fig tree. As soon as its branches are full of sap, and it is bursting into leaf, you know that summer is near.
33 Momwemonso, pamene mudzaona zinthu zonsezi mudzadziwe kuti ali pafupi pa khomo penipeni.
And so may you, as soon as you see all these things, know that he is at your doors.
34 Zoonadi, ndikuwuzani kuti mʼbado uwu sudzatha mpaka zinthu zonse zitachitika.
I tell you, even the present generation will not pass away, until all these things have taken place.
35 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
The heavens and the earth will pass away, but my words will never pass away.
36 “Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha.
But about that day and hour, no one knows – not even the angels of heaven, not even the Son – but only the Father himself.
37 Monga momwe zinalili nthawi ya Nowa, momwemonso zidzatero pobwera kwa Mwana wa Munthu.
For, just as in the days of Noah, so will it be at the coming of the Son of Man.
38 Pakuti masiku amenewo chisanafike chigumula, anthu amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo;
In those days before the flood they went on eating and drinking, marrying and being married, up to the very day on which Noah entered the ark,
39 ndipo sanadziwe za chimene chikanachitika mpaka pamene chigumula chinafika ndi kuwamiza onse. Umu ndi mmene zidzakhalira pobwera kwa Mwana wa Munthu.
taking not notice until the flood came and swept them one and all away; and so will it be at the coming of the Son of Man.
40 Amuna awiri adzakhala mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
At that time, of two men on a farm one will be taken and one left;
41 Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
of two women grinding with a hand-mill one will be taken and one left.
42 “Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera.
Therefore watch; for you cannot be sure on what day your Master is coming.
43 Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.
But this you do know, that, had the owner of the house known at what time of night the thief was coming, they would have been on the watch, and would not have allowed their house to be broken into.
44 Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.
Therefore, you must also prepare, since it is just when you are least expecting him that the Son of Man will come.
45 “Kodi wantchito wokhulupirika ndi wanzeru amene ambuye ake anamuyika kukhala woyangʼanira antchito a mʼnyumba kuti awapatse chakudya chawo pa nthawi yake ndani?
Who, then is that trustworthy, careful servant, who has been placed by their master over his household, to give them their food at the proper time?
46 Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi.
Happy will that servant be whom their master, when he comes home, will find doing this.
47 Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense.
I tell you that their master will put them in charge of the whole of his property.
48 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo ndi woyipa, nati kwa iye yekha, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera,’
But, should the servant be a bad servant, and say to themselves “My master is a long time in coming,”
49 nayamba kumenya antchito anzake, nadya ndi kumwa ndi zidakwa.
and begin to beat their fellow servants, and eat and drink with drunkards,
50 Mbuye wa wantchitoyo adzabwera pa tsiku limene iye samamuyembekezera ndi pa nthawi imene iye sakuyidziwa.
that servant’s master will come on a day when they do not expect him, and at an hour of which they are unaware,
51 Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
and will flog the servant severely, and assign them their place among the hypocrites, where there will be weeping and grinding of teeth.

< Mateyu 24 >