< Malaki 4 >

1 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi. 2 Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola. 3 Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 4 Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse. 5 “Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. 6 Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”

< Malaki 4 >