< Luka 20 >

1 Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
On one of those days, as he was teaching the people in the temple and preaching the Good News, the priests and scribes came to him with the elders.
2 Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?”
They asked him, “Tell us: by what authority do you do these things? Or who is giving you this authority?”
3 Iye anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe,
He answered them, “I also will ask you one question. Tell me:
4 ‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’”
the baptism of John, was it from heaven, or from men?”
5 Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’
They reasoned with themselves, saying, “If we say, ‘From heaven,’ he will say, ‘Why didn’t you believe him?’
6 Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.”
But if we say, ‘From men,’ all the people will stone us, for they are persuaded that John was a prophet.”
7 Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.”
They answered that they didn’t know where it was from.
8 Yesu anati, “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”
Jesus said to them, “Neither will I tell you by what authority I do these things.”
9 Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali.
He began to tell the people this parable: “A man planted a vineyard and rented it out to some farmers, and went into another country for a long time.
10 Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu.
At the proper season, he sent a servant to the farmers to collect his share of the fruit of the vineyard. But the farmers beat him and sent him away empty.
11 Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu.
He sent yet another servant, and they also beat him and treated him shamefully, and sent him away empty.
12 Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.
He sent yet a third, and they also wounded him and threw him out.
13 “Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’
The lord of the vineyard said, ‘What shall I do? I will send my beloved son. It may be that seeing him, they will respect him.’
14 “Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’
“But when the farmers saw him, they reasoned among themselves, saying, ‘This is the heir. Come, let’s kill him, that the inheritance may be ours.’
15 Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha. “Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa?
Then they threw him out of the vineyard and killed him. What therefore will the lord of the vineyard do to them?
16 Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.” Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.”
He will come and destroy these farmers, and will give the vineyard to others.” When they heard that, they said, “May that never be!”
17 Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti, “‘Mwala umene omanga nyumba anawukana wasanduka mwala wa pa ngodya.
But he looked at them and said, “Then what is this that is written, ‘The stone which the builders rejected was made the chief cornerstone’?
18 Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’”
Everyone who falls on that stone will be broken to pieces, but it will crush whomever it falls on to dust.”
19 Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.
The chief priests and the scribes sought to lay hands on him that very hour, but they feared the people—for they knew he had spoken this parable against them.
20 Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza.
They watched him and sent out spies, who pretended to be righteous, that they might trap him in something he said, so as to deliver him up to the power and authority of the governor.
21 Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi.
They asked him, “Teacher, we know that you say and teach what is right, and aren’t partial to anyone, but truly teach the way of God.
22 Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?”
Is it lawful for us to pay taxes to Caesar, or not?”
23 Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti,
But he perceived their craftiness, and said to them, “Why do you test me?
24 “Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”
Show me a denarius. Whose image and inscription are on it?” They answered, “Caesar’s.”
25 Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”
He said to them, “Then give to Caesar the things that are Caesar’s, and to God the things that are God’s.”
26 Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.
They weren’t able to trap him in his words before the people. They marveled at his answer and were silent.
27 Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso.
Some of the Sadducees came to him, those who deny that there is a resurrection.
28 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
They asked him, “Teacher, Moses wrote to us that if a man’s brother dies having a wife, and he is childless, his brother should take the wife and raise up children for his brother.
29 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana.
There were therefore seven brothers. The first took a wife, and died childless.
30 Wachiwiri
The second took her as wife, and he died childless.
31 ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana.
The third took her, and likewise the seven all left no children, and died.
32 Pa mapeto pake mkaziyo anafanso.
Afterward the woman also died.
33 Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?”
Therefore in the resurrection whose wife of them will she be? For the seven had her as a wife.”
34 Yesu anayankha kuti, “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa. (aiōn g165)
Jesus said to them, “The children of this age marry and are given in marriage. (aiōn g165)
35 Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. (aiōn g165)
But those who are considered worthy to attain to that age and the resurrection from the dead neither marry nor are given in marriage. (aiōn g165)
36 Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.
For they can’t die any more, for they are like the angels and are children of God, being children of the resurrection.
37 Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’
But that the dead are raised, even Moses showed at the bush, when he called the Lord ‘The God of Abraham, the God of Isaac, and the God of Jacob.’
38 Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”
Now he is not the God of the dead, but of the living, for all are alive to him.”
39 Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!”
Some of the scribes answered, “Teacher, you speak well.”
40 Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena.
They didn’t dare to ask him any more questions.
41 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide?
He said to them, “Why do they say that the Christ is David’s son?
42 Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti, “Ambuye anati kwa Ambuye anga: ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,
David himself says in the book of Psalms, ‘The Lord said to my Lord, “Sit at my right hand,
43 mpaka Ine nditasandutsa adani anu chopondapo mapazi anu?’
until I make your enemies the footstool of your feet.”’
44 Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”
“David therefore calls him Lord, so how is he his son?”
45 Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake,
In the hearing of all the people, he said to his disciples,
46 “Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando.
“Beware of those scribes who like to walk in long robes, and love greetings in the marketplaces, the best seats in the synagogues, and the best places at feasts;
47 Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”
who devour widows’ houses, and for a pretense make long prayers. These will receive greater condemnation.”

< Luka 20 >