< Luka 15 >

1 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake.
모든 세리와 죄인들이 말씀을 들으러 가까이 나아오니
2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.”
바리새인과 서기관들이 원망하여 가로되 이 사람이 죄인을 영접하고 음식을 같이 먹는다 하더라
3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili:
예수께서 저희에게 이 비유로 이르시되
4 “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza?
너희 중에 어느 사람이 양 일백 마리가 있는데 그 중에 하나를 잃으면 아흔아홉 마리를 들에 두고 그 잃은 것을 찾도록 찾아 다니지 아니하느냐
5 Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe
또 찾은즉 즐거워 어깨에 메고
6 ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’
집에 와서 그 벗과 이웃을 불러 모으고 말하되 나와 함께 즐기자 나의 잃은 양을 찾았노라 하리라
7 Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”
내가 너희에게 이르노니 이와 같이 죄인 하나가 회개하면 하늘에서는 회개할 것 없는 의인 아흔아홉을 인하여 기뻐하는 것보다 더하리라
8 “Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa nyale ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza?
어느 여자가 열 드라크마가 있는데 하나를 잃으면 등불을 켜고 집을 쓸며 찾도록 부지런히 찾지 아니하겠느냐
9 Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’
또 찾은즉 벗과 이웃을 불러 모으고 말하되 나와 함께 즐기자 잃은 드라크마를 찾았노라 하리라
10 Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”
내가 너희에게 이르노니 이와 같이 죄인 하나가 회개하면 하나님의 사자들 앞에 기쁨이 되느니라
11 Yesu anapitiriza kunena kuti, “Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri.
또 가라사대 어떤 사람이 두 아들이 있는데
12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.
그 둘째가 아비에게 말하되 아버지여 재산 중에서 내게 돌아올 분깃을 내게 주소서 하는지라 아비가 그 살림을 각각 나눠 주었더니
13 “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko.
그 후 며칠이 못되어 둘째 아들이 재산을 다 모아 가지고 먼 나라에 가 거기서 허랑방탕하여 그 재산을 허비하더니
14 Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka.
다 없이한 후 그 나라에 크게 훙년이 들어 저가 비로소 궁핍한지라
15 Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba.
가서 그 나라 백성 중 하나에게 붙여 사니 그가 저를 들로 보내어 돼지를 치게 하였는데
16 Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.
저가 돼지 먹는 쥐엄 열매로 배을 채우고자 하되 주는 자가 없는지라
17 “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala!
이에 스스로 돌이켜 가로되 내 아버지에게는 양식이 풍족한 품꾼이 얼마나 많은고 나는 여기서 주려 죽는구나
18 Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu.
내가 일어나 아버지께 가서 이르기를 아버지여 내가 하늘과 아버지께 죄를 얻었사오니
19 Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’
지금부터는 아버지의 아들이라 일컬음을 감당치 못하겠나이다 나를 품꾼의 하나로 보소서 하리라 하고
20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake. “Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.
이에 일어나서 아버지께 돌아 가니라 아직도 상거가 먼데 아버지가 저를 보고 측은히 여겨 달려가 목을 안고 입을 맞추니
21 “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’
아들이 가로되 아버지여 내가 하늘과 아버지께 죄를 얻었사오니 지금부터는 아버지의 아들이라 일컬음을 감당치 못하겠나이다 하나
22 “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato.
아버지는 종들에게 이르되 제일 좋은 옷을 내어다가 입히고 손에 가락지를 끼우고 발에 신을 신기라
23 Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera.
그리고 살진 송아지를 끌어다가 잡으라 우리가 먹고 즐기자
24 Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.
이 내 아들은 죽었다가 다시 살아났으며 내가 잃었다가 다시 얻었노라 하니 저희가 즐거워하더라
25 “Nthawi imeneyi, mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Iye atafika pafupi ndi nyumba, anamva anthu akuyimba ndi kuvina.
맏아들은 밭에 있다가 돌아와 집에 가까웠을 때에 풍류와 춤추는 소리를 듣고
26 Ndipo iye anayitana mmodzi wa antchito, namufunsa chimene chimachitika.
한 종을 불러 이 무슨 일인가 물은대
27 Iye anayankha kuti, ‘Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.’
대답하되 당신의 동생이 돌아왔으매 당신의 아버지가 그의 건강한 몸을 다시 맞아 들이게 됨을 인하여 살진 송아지를 잡았나이다 하니
28 “Mwana wamkulu anakwiya ndipo anakana kulowa. Chomwecho abambo ake anatuluka ndi kumudandaulira.
저가 노하여 들어가기를 즐겨 아니하거늘 아버지가 나와서 권한대
29 Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga.
아버지께 대답하여 가로되 내가 여러 해 아버지를 섬겨 명을 어김이 없거늘 내게는 염소 새끼라도 주어 나와 내 벗으로 즐기게 하신 일이 없더니
30 Koma pamene mwana wanu uyu amene wawononga chuma chanu ndi achiwerewere wabwera ku nyumba, inu mwamuphera mwana wangʼombe wonenepa.’”
아버지의 살림을 창기와 함께 먹어버린 이 아들이 돌아오매 이를 위하여 살진 송아지를 잡으셨나이다
31 Abambowo anati, “Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine nthawi zonse ndipo zonse ndili nazo ndi zako.
아버지가 이르되 얘 너는 항상 나와 함께 있으니 내 것이 다 네 것이로되
32 Koma tinayenera kukondwera ndi kusangalala, chifukwa mʼbale wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyonso; iye anali wotayika ndipo wapezeka.”
이 네 동생은 죽었다가 살았으며 내가 잃었다가 얻었기로 우리가 즐거워하고 기뻐하는 것이 마땅하다 하니라

< Luka 15 >