< Luka 13 >

1 Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo.
正当那时,有人将彼拉多使加利利人的血搀杂在他们祭物中的事告诉耶稣。
2 Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewa anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa anavutika mʼnjira iyi?
耶稣说:“你们以为这些加利利人比众加利利人更有罪,所以受这害吗?
3 Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.
我告诉你们,不是的!你们若不悔改,都要如此灭亡!
4 Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu?
从前西罗亚楼倒塌了,压死十八个人;你们以为那些人比一切住在耶路撒冷的人更有罪吗?
5 Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.”
我告诉你们,不是的!你们若不悔改,都要如此灭亡!”
6 Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze.
于是用比喻说:“一个人有一棵无花果树栽在葡萄园里。他来到树前找果子,却找不着。
7 Tsono kwa munthu amene amasamalira munda wamphesawo anati, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna chipatso pa mtengo uwu ndipo sindinachipeze. Udule! Nʼchifukwa chiyani ukuwononga nthaka?’
就对管园的说:‘看哪,我这三年来到这无花果树前找果子,竟找不着。把它砍了吧,何必白占地土呢!’
8 “Munthuyo anayankha kuti, ‘Bwana, tawusiyani kwa chaka chimodzi chokha ndipo ine ndikumba ngalande mozungulira ndi kuthira manyowa.
管园的说:‘主啊,今年且留着,等我周围掘开土,加上粪;
9 Ngati udzabale zipatso chaka chamawa, zili bwino! Koma ngati sudzabala, pamenepo mudzawudule.’”
以后若结果子便罢,不然再把它砍了。’”
10 Pa Sabata Yesu ankaphunzitsa mʼsunagoge ina,
安息日,耶稣在会堂里教训人。
11 ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe.
有一个女人被鬼附着,病了十八年,腰弯得一点直不起来。
12 Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, “Amayi, mwamasulidwa ku mavuto.”
耶稣看见,便叫过她来,对她说:“女人,你脱离这病了!”
13 Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.
于是用两只手按着她;她立刻直起腰来,就归荣耀与 神。
14 Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.”
管会堂的因为耶稣在安息日治病,就气忿忿地对众人说:“有六日应当做工;那六日之内可以来求医,在安息日却不可。”
15 Ambuye anamuyankha kuti, “Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi?
主说:“假冒为善的人哪,难道你们各人在安息日不解开槽上的牛、驴,牵去饮吗?
16 Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”
况且这女人本是亚伯拉罕的后裔,被撒但捆绑了这十八年,不当在安息日解开她的绑吗?”
17 Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita.
耶稣说这话,他的敌人都惭愧了;众人因他所行一切荣耀的事,就都欢喜了。
18 Kenaka Yesu anafunsa kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani?
耶稣说:“神的国好像什么?我拿什么来比较呢?
19 Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”
好像一粒芥菜种,有人拿去种在园子里,长大成树,天上的飞鸟宿在它的枝上。”
20 Iye anafunsanso kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani?
又说:“我拿什么来比 神的国呢?
21 Uli ngati yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza ndi ufa wambiri mpaka anafufumitsa ufawo.”
好比面酵,有妇人拿来藏在三斗面里,直等全团都发起来。”
22 Ndipo Yesu anayendayenda mʼmizinda ndi mʼmidzi, kumaphunzitsa pamene Iye ankapita ku Yerusalemu.
耶稣往耶路撒冷去,在所经过的各城各乡教训人。
23 Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti,
有一个人问他说:“主啊,得救的人少吗?”
24 “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.
耶稣对众人说:“你们要努力进窄门。我告诉你们,将来有许多人想要进去,却是不能。
25 Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’ “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’
及至家主起来关了门,你们站在外面叩门,说:‘主啊,给我们开门!’他就回答说:‘我不认识你们,不晓得你们是哪里来的!’
26 “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.
那时,你们要说:‘我们在你面前吃过喝过,你也在我们的街上教训过人。’
27 “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’
他要说:‘我告诉你们,我不晓得你们是哪里来的。你们这一切作恶的人,离开我去吧!’
28 “Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja.
你们要看见亚伯拉罕、以撒、雅各,和众先知都在 神的国里,你们却被赶到外面,在那里必要哀哭切齿了。
29 Anthu adzachokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kummwera, kudzakhala pa phwando mu ufumu wa Mulungu.
从东、从西、从南、从北将有人来,在 神的国里坐席。
30 Ndithudi otsirizira ndiye adzakhale oyambirira, ndipo oyambirira ndiye adzakhale otsirizira.”
只是有在后的,将要在前;有在前的,将要在后。”
31 Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.”
正当那时,有几个法利赛人来对耶稣说:“离开这里去吧,因为希律想要杀你。”
32 Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.”
耶稣说:“你们去告诉那个狐狸说:‘今天、明天我赶鬼治病,第三天我的事就成全了。’
33 Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.
虽然这样,今天、明天、后天,我必须前行,因为先知在耶路撒冷之外丧命是不能的。
34 Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune!
耶路撒冷啊!耶路撒冷啊!你常杀害先知,又用石头打死那奉差遣到你这里来的人。我多次愿意聚集你的儿女,好像母鸡把小鸡聚集在翅膀底下;只是你们不愿意。
35 Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”
看哪,你们的家成为荒场留给你们。我告诉你们,从今以后你们不得再见我,直等到你们说:‘奉主名来的是应当称颂的。’”

< Luka 13 >