< Luka 10 >

1 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako.
Post hæc autem designavit Dominus et alios septuaginta duos. et misit illos binos ante faciem suam in omnem civitatem, et locum, quo erat ipse venturus.
2 Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola.
Et dicebat illis: Messis quidem multa, operarii autem pauci. Rogate ergo dominum messis ut mittat operarios in messem suam.
3 Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu.
Ite: ecce ego mitto vos sicut agnos inter lupos.
4 Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira.
Nolite portare sacculum, neque peram, neque calceamenta, et neminem per viam salutaveritis.
5 “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’
In quamcumque domum intraveritis, primum dicite: Pax huic domui:
6 Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu.
et si ibi fuerit filius pacis, requiescet super illum pax vestra: sin autem, ad vos revertetur.
7 Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina.
In eadem autem domo manete edentes, et bibentes quæ apud illos sunt: dignus est enim operarius mercede sua. Nolite transire de domo in domum.
8 “Mukamalowa mʼmudzi, ndi kulandiridwa, idyani chilichonse akukonzerani.
Et in quamcumque civitatem intraveritis, et susceperint vos, manducate quæ apponuntur vobis:
9 Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’
et curate infirmos, qui in illa sunt, et dicite illis: Appropinquavit in vos regnum Dei.
10 Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti,
In quamcumque autem civitatem intraveritis, et non susceperint vos, exeuntes in plateas eius, dicite:
11 ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’
Etiam pulverem, qui adhæsit nobis de civitate vestra, extergimus in vos: tamen hoc scitote, quia appropinquavit regnum Dei.
12 Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo.
Dico vobis, quia Sodomis in die illa remissius erit, quam illi civitati.
13 “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa.
Væ tibi Corozain, væ tibi Bethsaida: quia si in Tyro, et Sidone factæ fuissent virtutes, quæ factæ sunt in vobis, olim in cilicio, et cinere sedentes pœniterent.
14 Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu.
Verumtamen Tyro, et Sidoni remissius erit in iudicio, quam vobis.
15 Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. (Hadēs g86)
Et tu Capharnaum usque ad cælum exaltata, usque ad infernum demergeris. (Hadēs g86)
16 “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”
Qui vos audit, me audit: et qui vos spernit, me spernit. Qui autem me spernit, spernit eum, qui misit me.
17 Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.”
Reversi sunt autem septuaginta duo cum gaudio, dicentes: Domine, etiam dæmonia subiiciuntur nobis in nomine tuo.
18 Iye anayankha kuti, “Ndinaona Satana akugwa kuchokera kumwamba ngati mphenzi.
Et ait illis: Videbam satanam sicut fulgor de cælo cadentem.
19 Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani.
Ecce dedi vobis potestatem calcandi supra serpentes, et scorpiones, et super omnem virtutem inimici: et nihil vobis nocebit.
20 Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.”
Verumtamen in hoc nolite gaudere quia spiritus vobis subiiciuntur: gaudete autem, quod nomina vestra scripta sunt in cælis.
21 Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.
In ipsa hora exultavit Spiritu sancto, et dixit: Confiteor tibi pater, Domine cæli et terræ, quod abscondisti hæc a sapientibus, et prudentibus, et revelasti ea parvulis. Etiam Pater: quoniam sic placuit ante te.
22 “Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”
Omnia mihi tradita sunt a Patre meo. Et nemo scit quis sit Filius, nisi Pater: et quis sit Pater, nisi Filius, et cui voluerit Filius revelare.
23 Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi.
Et conversus ad discipulos suos, dixit: Beati oculi, qui vident quæ vos videtis.
24 Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”
Dico enim vobis, quod multi prophetæ, et reges voluerunt videre quæ vos videtis, et non viderunt: et audire quæ auditis, et non audierunt.
25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” (aiōnios g166)
Et ecce quidam Legisperitus surrexit tentans illum, et dicens: Magister, quid faciendo vitam æternam possidebo? (aiōnios g166)
26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”
At ille dixit ad eum: In lege quid scriptum est? quomodo legis?
27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
Ille respondens dixit: Diliges Dominum Deum tuum ex toto corde tuo, et ex tota anima tua, et ex omnibus virtutibus tuis, et ex omni mente tua: et proximum tuum sicut teipsum.
28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”
Dixitque illi: Recte respondisti: hoc fac, et vives.
29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”
Ille autem volens iustificare seipsum, dixit ad Iesum: Et quis est meus proximus?
30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa.
Suscipiens autem Iesus, dixit: Homo quidam descendebat ab Ierusalem in Iericho, et incidit in latrones, qui etiam despoliaverunt eum: et plagis impositis abierunt semivivo relicto.
31 Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala.
Accidit autem ut sacerdos quidam descenderet eadem via: et viso illo præterivit.
32 Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso.
Similiter et Levita, cum esset secus locum, et videret eum, pertransiit.
33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni.
Samaritanus autem quidam iter faciens, venit secus eum: et videns eum, misericordia motus est.
34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira.
Et appropians alligavit vulnera eius, infundens oleum, et vinum: et imponens illum in iumentum suum, duxit in stabulum, et curam eius egit.
35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’
Et altera die protulit duos denarios, et dedit stabulario, et ait: Curam illius habe: et quodcumque supererogaveris, ego cum rediero reddam tibi.
36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”
Quis horum trium videtur tibi proximus fuisse illi, qui incidit in latrones?
37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.” Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”
At ille dixit: Qui fecit misericordiam in illum. Et ait illi Iesus: Vade, et tu fac similiter.
38 Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake.
Factum est autem, dum irent, et ipse intravit in quoddam castellum: et mulier quædam Martha nomine, excepit illum in domum suam,
39 Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena.
et huic erat soror nomine Maria, quæ etiam sedens secus pedes Domini, audiebat verbum illius.
40 Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!”
Martha autem satagebat circa frequens ministerium: quæ stetit, et ait: Domine, non est tibi curæ quod soror mea reliquit me solam ministrare? dic ergo illi, ut me adiuvet.
41 Ambuye anati, “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri,
Et respondens dixit illis Dominus: Martha, Martha, sollicita es, et turbaris erga plurima.
42 koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”
Porro unum est necessarium. Maria optimam partem elegit, quæ non auferetur ab ea.

< Luka 10 >