< Yoswa 12 >

1 Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa: 2 Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. 3 Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga. 4 Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. 5 Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. 6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo. 7 Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. 8 Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa: 9 mfumu ya Yeriko imodzi mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi 10 mfumu ya Yerusalemu imodzi mfumu ya Hebroni imodzi 11 mfumu ya Yarimuti imodzi mfumu ya Lakisi imodzi 12 mfumu ya Egiloni imodzi mfumu ya Gezeri imodzi 13 mfumu ya Debri imodzi mfumu ya Gederi imodzi 14 mfumu ya Horima imodzi mfumu ya Aradi imodzi 15 mfumu ya Libina imodzi mfumu ya Adulamu imodzi 16 mfumu ya Makeda imodzi mfumu ya Beteli imodzi 17 mfumu ya Tapuwa imodzi mfumu ya Heferi imodzi 18 mfumu ya Afeki imodzi mfumu ya Lasaroni imodzi 19 mfumu ya Madoni imodzi mfumu ya Hazori imodzi 20 mfumu ya Simuroni Meroni imodzi mfumu ya Akisafu imodzi 21 mfumu ya Taanaki imodzi mfumu ya Megido imodzi 22 mfumu ya Kadesi imodzi mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi 23 mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi 24 mfumu ya Tiriza imodzi mafumu onse pamodzi analipo 31.

< Yoswa 12 >