< Yobu 25 >

1 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
書亞人比勒達回答說:
2 “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.
上帝有治理之權,有威嚴可畏; 他在高處施行和平。
3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?
他的諸軍豈能數算? 他的光亮一發,誰不蒙照呢?
4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?
這樣在上帝面前,人怎能稱義? 婦人所生的怎能潔淨?
5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,
在上帝眼前,月亮也無光亮, 星宿也不清潔。
6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi, mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”
何況如蟲的人, 如蛆的世人呢!

< Yobu 25 >