< Yesaya 63 >

1 Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu, atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira? Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola, akuyenda mwa mphamvu zake? “Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”
這從以東的波斯拉來, 穿紅衣服, 裝扮華美, 能力廣大, 大步行走的是誰呢? 就是我, 是憑公義說話, 以大能施行拯救。
2 Nanga bwanji zovala zanu zili psuu, ngati za munthu wofinya mphesa?
你的裝扮為何有紅色? 你的衣服為何像踹酒醡的呢?
3 “Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, palibe ndi mmodzi yemwe anali nane. Ndinawapondereza ndili wokwiya ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali; magazi awo anadothera pa zovala zanga, ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
我獨自踹酒醡; 眾民中無一人與我同在。 我發怒將他們踹下, 發烈怒將他們踐踏。 他們的血濺在我衣服上, 並且污染了我一切的衣裳。
4 Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga; ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
因為,報仇之日在我心中; 救贖我民之年已經來到。
5 Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza. Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza; choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga, ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
我仰望,見無人幫助; 我詫異,沒有人扶持。 所以,我自己的膀臂為我施行拯救; 我的烈怒將我扶持。
6 Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya; ndipo ndinawasakaza ndipo ndinathira magazi awo pansi.”
我發怒,踹下眾民; 發烈怒,使他們沉醉, 又將他們的血倒在地上。
7 Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova, ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa. Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira. Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake Yehova wachitira nyumba ya Israeli zinthu zabwino zambiri.
我要照耶和華一切所賜給我們的, 提起他的慈愛和美德, 並他向以色列家所施的大恩; 這恩是照他的憐恤 和豐盛的慈愛賜給他們的。
8 Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga, ana anga amene sadzandinyenga Ine.” Choncho anawapulumutsa.
他說:他們誠然是我的百姓, 不行虛假的子民; 這樣,他就作了他們的救主。
9 Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse, ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa. Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa, anawanyamula ndikuwatenga kuyambira kale lomwe.
他們在一切苦難中, 他也同受苦難; 並且他面前的使者拯救他們; 他以慈愛和憐憫救贖他們; 在古時的日子常保抱他們,懷搋他們。
10 Komabe iwo anawukira ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
他們竟悖逆,使主的聖靈擔憂。 他就轉作他們的仇敵, 親自攻擊他們。
11 Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana, masiku a Mose mtumiki wake; ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja, pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo? Ali kuti Iye amene anayika Mzimu Woyera pakati pawo?
那時,他們想起古時的日子- 摩西和他百姓,說: 將百姓和牧養他全群的人 從海裏領上來的在哪裏呢? 將他的聖靈降在他們中間的在哪裏呢?
12 Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
使他榮耀的膀臂在摩西的右手邊行動, 在他們前面將水分開, 要建立自己永遠的名,
13 amene anawayendetsa pa nyanja yozama? Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu, iwo sanapunthwe;
帶領他們經過深處, 如馬行走曠野, 使他們不致絆跌的在哪裏呢?
14 Mzimu Woyera unawapumulitsa ngati mmene ngʼombe zimapumulira. Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu kuti dzina lanu lilemekezeke.”
耶和華的靈使他們得安息, 彷彿牲畜下到山谷; 照樣,你也引導你的百姓, 要建立自己榮耀的名。
15 Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka, wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife. Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti? Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.
求你從天上垂顧, 從你聖潔榮耀的居所觀看。 你的熱心和你大能的作為在哪裏呢? 你愛慕的心腸和憐憫向我們止住了。
16 Koma Inu ndinu Atate athu, ngakhale Abrahamu satidziwa kapena Israeli kutivomereza ife; Inu Yehova, ndinu Atate athu, kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
亞伯拉罕雖然不認識我們, 以色列也不承認我們, 你卻是我們的父。 耶和華啊,你是我們的父; 從萬古以來,你名稱為「我們的救贖主」。
17 Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu? Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso? Bwererani chifukwa cha atumiki anu; mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.
耶和華啊,你為何使我們走差離開你的道, 使我們心裏剛硬、不敬畏你呢? 求你為你僕人, 為你產業支派的緣故,轉回來。
18 Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa, adani athu anasakaza malo anu opatulika.
你的聖民不過暫時得這產業; 我們的敵人已經踐踏你的聖所。
19 Ife tili ngati anthu amene simunawalamulirepo ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.
我們好像你未曾治理的人, 又像未曾得稱你名下的人。

< Yesaya 63 >