< Yesaya 36 >

1 Chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya ku Yuda, nayilanda.
希西家王十四年,亞述王西拿基立上來攻擊猶大的一切堅固城,將城攻取。
2 Kenaka mfumu ya ku Asiriya inatuma kazembe wake wankhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo kuchokera ku Lakisi kupita kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo anayima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe lakumtunda pa msewu wopita ku malo a munda wa mmisiri wochapa zovala.
亞述王從拉吉差遣拉伯沙基率領大軍往耶路撒冷,到希西家王那裏去。他就站在上池的水溝旁,在漂布地的大路上。
3 Panali anthu atatu. Woyamba anali Eliyakimu mwana wa Hilikiya komanso ndiye woyangʼanira nyumba ya mfumu. Wachiwiri anali Sebina amene anali mlembi wa bwalo; ndipo wachitatu anali Yowa mwana wa Asafu komanso anali wolemba zochitika. Anthu awa anatuluka kukakumana ndi kazembe wa ankhondo uja.
於是希勒家的兒子家宰以利亞敬,並書記舍伯那和亞薩的兒子史官約亞,出來見拉伯沙基。
4 Kazembe wa ankhondo anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti, “Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?
拉伯沙基對他們說:「你們去告訴希西家說,亞述大王如此說:『你所倚靠的有甚麼可仗賴的呢?
5 Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine?
你說,有打仗的計謀和能力,我看不過是虛話。你到底倚靠誰才背叛我呢?
6 Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.
看哪,你所倚靠的埃及是那壓傷的葦杖,人若靠這杖,就必刺透他的手。埃及王法老向一切倚靠他的人也是這樣。
7 Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’
你若對我說:我們倚靠耶和華-我們的上帝。希西家豈不是將上帝的邱壇和祭壇廢去,且對猶大和耶路撒冷的人說:你們當在這壇前敬拜嗎?
8 “Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo!
現在你把當頭給我主亞述王,我給你二千匹馬,看你這一面騎馬的人夠不夠。
9 Iwe ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo.
若不然,怎能打敗我主臣僕中最小的軍長呢?你竟倚靠埃及的戰車馬兵嗎?
10 Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.”
現在我上來攻擊毀滅這地,豈沒有耶和華的意思嗎?耶和華吩咐我說,你上去攻擊毀滅這地吧!』」
11 Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa anawuza kazembeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
以利亞敬、舍伯那、約亞對拉伯沙基說:「求你用亞蘭言語和僕人說話,因為我們懂得;不要用猶大言語和我們說話,達到城上百姓的耳中。」
12 Koma kazembeyo anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
拉伯沙基說:「我主差遣我來,豈是單對你和你的主說這些話嗎?不也是對這些坐在城上、要與你們一同吃自己糞喝自己尿的人說嗎?」
13 Tsono kazembeyo anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya!
於是,拉伯沙基站着,用猶大言語大聲喊着說:「你們當聽亞述大王的話。
14 Zimene mfumu ikunena ndi izi: Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni!
王如此說:『你們不要被希西家欺哄了,因他不能拯救你們。
15 Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
也不要聽希西家使你們倚靠耶和華說:耶和華必要拯救我們,這城必不交在亞述王的手中。』
16 “Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake,
不要聽希西家的話,因亞述王如此說:『你們要與我和好。出來投降我,各人就可以吃自己葡萄樹和無花果樹的果子,喝自己井裏的水。
17 mpaka mfumuyo itabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanulo, dziko limene lili ndi tirigu ndi vinyo watsopano, dziko loyenda mkaka ndi uchi.
等我來領你們到一個地方,與你們本地一樣,就是有五穀和新酒之地,有糧食和葡萄園之地。
18 “Inu musalole kuti Hezekiya akusocheretseni pamene iye akuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi alipo mulungu wa anthu a mtundu wina amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya?
你們要謹防,恐怕希西家勸導你們說:耶和華必拯救我們。列國的神有哪一個救他本國脫離亞述王的手呢?
19 Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa?
哈馬和亞珥拔的神在哪裏呢?西法瓦音的神在哪裏呢?他們曾救撒馬利亞脫離我的手嗎?
20 Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
這些國的神有誰曾救自己的國脫離我的手呢?難道耶和華能救耶路撒冷脫離我的手嗎?』」
21 Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”
百姓靜默不言,並不回答一句,因為王曾吩咐說:「不要回答他。」
22 Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu; Sebina mlembi wa bwalo; ndi Yowa, mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza zonse zimene anayankhula kazembe uja.
當下希勒家的兒子家宰以利亞敬和書記舍伯那,並亞薩的兒子史官約亞,都撕裂衣服,來到希西家那裏,將拉伯沙基的話告訴了他。

< Yesaya 36 >