< Yesaya 15 >

1 Uthenga wonena za Mowabu: Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. Mzinda wa Kiri wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. 2 Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo, akupita ku malo awo achipembedzo kukalira; anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndipo ndevu zonse zametedwa. 3 Mʼmisewu akuvala ziguduli; pa madenga ndi mʼmabwalo aliyense akulira mofuwula, misozi ili pupupu. 4 Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula, mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi. Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula, ndipo ataya mtima. 5 Inenso ndikulirira Mowabu; chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari ndi Egilati-Selisiya akupita akulira ku chikweza cha Luhiti, Akulira mosweka mtima pa njira yopita ku Horonaimu; akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo. 6 Madzi a ku Nimurimu aphwa ndipo udzu wauma; zomera zawonongeka ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala. 7 Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga, achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi. 8 Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu; kulira kwawo kosweka mtima kukumveka mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu. 9 Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi, komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni, mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.

< Yesaya 15 >