< Yesaya 12 >

1 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati: “Ndikukuyamikani, Inu Yehova; chifukwa ngakhale munandipsera mtima, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mwanditonthoza. 2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga; ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.” 3 Mudzakondwera popeza Yehova ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu. 4 Tsiku limenelo mudzati: “Yamikani Yehova, tamandani dzina lake; mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. 5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu; zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi. 6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”

< Yesaya 12 >