< Genesis 27 >

1 Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.” Iye anayankha, “Ine abambo.”
And it came to pass, that when Isaac was old, and his eyes were dim, so that he could not see, he called Esau his eldest son, and said unto him, My son: and he said unto him, Behold, here am I.
2 Isake anati, “Tsopano ine ndakalamba, ndipo sindidziwa tsiku langa lakufa.
And he said, Behold now, I am old, I know not the day of my death:
3 Tsono tenga zida zako, muvi wako ndi uta, pita kuthengo ukandiphere nyama.
Now therefore take, I pray you, your weapons, your quiver and your bow, and go out to the field, and take me some venison;
4 Undikonzere chakudya chabwino monga muja ndimakonderamu ndipo ubwere nacho kwa ine kuti ndidye ndi kuti ndikudalitse ndisanamwalire.”
And make me savoury food, such as I love, and bring it to me, that I may eat; that my soul may bless you before I die.
5 Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama,
And Rebekah heard when Isaac spoke to Esau his son. And Esau went to the field to hunt for venison, and to bring it.
6 Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti,
And Rebekah spoke unto Jacob her son, saying, Behold, I heard your father speak unto Esau your brother, saying,
7 ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’
Bring me venison, and make me savoury food, that I may eat, and bless you before the LORD before my death.
8 Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze:
Now therefore, my son, obey my voice according to that which I command you.
9 Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera.
Go now to the flock, and fetch me from thence two good kids of the goats; and I will make them savoury food for your father, such as he loves:
10 Kenaka upite nacho chakudyacho kwa abambo ako kuti adye ndi kukudalitsa asanafe.”
And you shall bring it to your father, that he may eat, and that he may bless you before his death.
11 Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala.
And Jacob said to Rebekah his mother, Behold, Esau my brother is a hairy man, and I am a smooth man:
12 Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.”
My father possibly will feel me, and I shall seem to him as a deceiver; and I shall bring a curse upon me, and not a blessing.
13 Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.”
And his mother said unto him, Upon me be your curse, my son: only obey my voice, and go fetch me them.
14 Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera.
And he went, and fetched, and brought them to his mother: and his mother made savoury food, such as his father loved.
15 Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo.
And Rebekah took goodly raiment of her eldest son Esau, which were with her in the house, and put them upon Jacob her younger son:
16 Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi.
And she put the skins of the kids of the goats upon his hands, and upon the smooth of his neck:
17 Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi.
And she gave the savoury food and the bread, which she had prepared, into the hand of her son Jacob.
18 Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.” Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”
And he came unto his father, and said, My father: and he said, Here am I; who are you, my son?
19 Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”
And Jacob said unto his father, I am Esau your first born; I have done according as you bade me: arise, I pray you, sit and eat of my venison, that your soul may bless me.
20 Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?” Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”
And Isaac said unto his son, How is it that you have found it so quickly, my son? And he said, Because the LORD your God brought it to me.
21 Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”
And Isaac said unto Jacob, Come near, I pray you, that I may feel you, my son, whether you be my very son Esau or not.
22 Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.”
And Jacob went near unto Isaac his father; and he felt him, and said, The voice is Jacob's voice, but the hands are the hands of Esau.
23 Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa.
And he discerned him not, because his hands were hairy, as his brother Esau's hands: so he blessed him.
24 Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobo anayankha, “Inde ndine.”
And he said, Are you my very son Esau? And he said, I am.
25 Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.” Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa.
And he said, Bring it near to me, and I will eat of my son's venison, that my soul may bless you. And he brought it near to him, and he did eat: and he brought him wine and he drank.
26 Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.”
And his father Isaac said unto him, Come near now, and kiss me, my son.
27 Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati, “Haa, fungo la mwana wanga lili ngati fungo la munda umene Yehova waudalitsa.
And he came near, and kissed him: and he smelled the smell of his raiment, and blessed him, and said, See, the smell of my son is as the smell of a field which the LORD has blessed:
28 Mulungu akugwetsere mame akumwamba ndipo minda yako ibale tirigu wambiri ndi vinyo watsopano.
Therefore God give you of the dew of heaven, and the fatness of the earth, and plenty of corn and wine:
29 Mitundu ya anthu ikutumikire iwe ndipo anthu akugwadire iwe. Ukhale wolamula abale ako, ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire. Amene akutemberera iwe atembereredwe ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”
Let people serve you, and nations bow down to you: be lord over your brethren, and let your mother's sons bow down to you: cursed be every one that curses you, and blessed be he that blesses you.
30 Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja.
And it came to pass, as soon as Isaac had made an end of blessing Jacob, and Jacob was yet scarce gone out from the presence of Isaac his father, that Esau his brother came in from his hunting.
31 Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”
And he also had made savoury food, and brought it unto his father, and said unto his father, Let my father arise, and eat of his son's venison, that your soul may bless me.
32 Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?” Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”
And Isaac his father said unto him, Who are you? And he said, I am your son, your firstborn Esau.
33 Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”
And Isaac trembled very exceedingly, and said, Who? where is he that has taken venison, and brought it me, and I have eaten of all before you came, and have blessed him? yea, and he shall be blessed.
34 Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”
And when Esau heard the words of his father, he cried with a great and exceeding bitter cry, and said unto his father, Bless me, even me also, O my father.
35 Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”
And he said, Your brother came with subtlety, and has taken away your blessing.
36 Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”
And he said, Is not he rightly named Jacob? for he has supplanted me these two times: he took away my birthright; and, behold, now he has taken away my blessing. And he said, Have you not reserved a blessing for me?
37 Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”
And Isaac answered and said unto Esau, Behold, I have made him your lord, and all his brethren have I given to him for servants; and with corn and wine have I sustained him: and what shall I do now unto you, my son?
38 Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.
And Esau said unto his father, Have you but one blessing, my father? bless me, even me also, O my father. And Esau lifted up his voice, and wept.
39 Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti, “Malo ako okhalapo sadzabala dzinthu, ndipo mvula sidzagwa pa minda yako.
And Isaac his father answered and said unto him, Behold, your dwelling shall be the fatness of the earth, and of the dew of heaven from above;
40 Udzakhala ndi moyo podalira lupanga ndipo udzatumikira mʼbale wako. Koma idzafika nthawi pamene udzakhala mfulu udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.”
And by your sword shall you live, and shall serve your brother; and it shall come to pass when you shall have the dominion, that you shall break his yoke from off your neck.
41 Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”
And Esau hated Jacob because of the blessing wherewith his father blessed him: and Esau said in his heart, The days of mourning for my father are at hand; then will I slay my brother Jacob.
42 Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire.
And these words of Esau her elder son were told to Rebekah: and she sent and called Jacob her younger son, and said unto him, Behold, your brother Esau, as concerning you, does comfort himself, purposing to kill you.
43 Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani.
Now therefore, my son, obey my voice; arise, flee you to Laban my brother to Haran;
44 Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika.
And tarry with him a few days, until your brother's fury turn away;
45 Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”
Until your brother's anger turn away from you, and he forget that which you have done to him: then I will send, and fetch you from thence: why should I be deprived also of you both in one day?
46 Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.”
And Rebekah said to Isaac, I am weary of my life because of the daughters of Heth: if Jacob take a wife of the daughters of Heth, such as these which are of the daughters of the land, what good shall my life do me?

< Genesis 27 >