< Ezara 2 >

1 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2 Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere: 3 Zidzukulu za Parosi 2,172 4 zidzukulu za Sefatiya 372 5 zidzukulu za Ara 775 6 zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) 2,812 7 zidzukulu za Elamu 1,254 8 zidzukulu za Zatu 945 9 zidzukulu za Zakai 760 10 zidzukulu za Bani 642 11 zidzukulu za Bebai 623 12 zidzukulu za Azigadi 1,222 13 zidzukulu za Adonikamu 666 14 zidzukulu za Bigivai 2,056 15 zidzukulu za Adini 454 16 zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98 17 zidzukulu za Bezayi 323 18 zidzukulu za Yora 112 19 zidzukulu za Hasumu 223 20 zidzukulu za Gibari 95. 21 Anthu a ku Betelehemu 123 22 Anthu aamuna a ku Netofa 56 23 Anthu aamuna a ku Anatoti 128 24 Anthu aamuna a ku Azimaveti 42 25 Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti 743 26 Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba 621 27 Anthu aamuna a ku Mikimasi 122 28 Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai 223 29 Anthu aamuna a ku Nebo 52 30 Anthu aamuna a ku Magaibisi 156 31 Anthu aamuna a ku Elamu wina 1,254 32 Anthu aamuna a ku Harimu 320 33 Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono 725 34 Anthu aamuna a ku Yeriko 345 35 Anthu aamuna a ku Sena 3,630. 36 Ansembe anali awa: Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) 973 37 Zidzukulu za Imeri 1,052 38 Zidzukulu za Pasuri 1,247 39 Zidzukulu za Harimu 1,017. 40 Alevi anali awa: Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) 74. 41 Anthu oyimba nyimbo anali awa: Zidzukulu za Asafu 128. 42 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai 139. 43 Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, 44 zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni, 45 zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu, 46 zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani, 47 zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya, 48 zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu, 49 zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai, 50 zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu, 51 zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, 52 zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, 53 zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema, 54 zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa. 55 Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu za Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda, 56 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, 57 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami. 58 Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali 392. 59 Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi: 60 Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali 652. 61 Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu za Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.) 62 Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63 Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu. 64 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65 kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66 Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67 ngamira 435 ndi abulu 6,720. 68 Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69 Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100. 70 Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.

< Ezara 2 >