< Eksodo 22 >

1 “Ngati munthu aba ngʼombe kapena nkhosa ndi kuyipha kapena kuyigulitsa, iye abweze ngʼombe zisanu pa ngʼombe imodzi ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi.
Si quis furatus fuerit bovem aut ovem, et occiderit vel vendiderit: quinque boves pro uno bove restituet, et quatuor oves pro una ove.
2 “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe.
Si effringens fur domum sive suffodiens fuerit inventus, et accepto vulnere mortuus fuerit, percussor non erit reus sanguinis.
3 Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo.
Quod si orto sole hoc fecerit, homicidium perpetravit, et ipse morietur. Si non habuerit quod pro furto reddat, ipse venundabitur.
4 “Ngati chiweto chobedwacho chipezeka chamoyo mʼmanja mwake, kaya ndi ngʼombe kapena bulu kapena nkhosa, mbalayo ibwezere ziweto ziwiri pa chiweto chobedwacho.
Si inventum fuerit apud eum quod furatus est, vivens: sive bos, sive asinus, sive ovis, duplum restituet.
5 “Ngati munthu alekerera ziweto zake kukalowa mʼmunda wa munthu wina kukadya mbewu zake, munthuyo amubwezere mwini mundawo mbewu zina zabwino kapena mpesa wina wabwino kwambiri.
Si læserit quispiam agrum vel vineam, et dimiserit jumentum suum ut depascatur aliena: quidquid optimum habuerit in agro suo, vel in vinea, pro damni æstimatione restituet.
6 “Ngati munthu ayatsa moto, motowo ndikukafika mpaka ku munda ndi kuwotcha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula, kapena munda wonse, ndiye kuti munthu amene anayatsa motoyo alipire.
Si egressus ignis invenerit spinas, et comprehenderit acervos frugum, sive stantes segetes in agris, reddet damnum qui ignem succenderit.
7 “Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho.
Si quis commendaverit amico pecuniam aut vas in custodiam, et ab eo, qui susceperat, furto ablata fuerint: si invenitur fur, duplum reddet:
8 Koma ngati mbalayo sipezeka, mwini nyumbayo ayenera kukaonekera ku bwalo lamilandu kuti akamve ngati anaba katundu wa mnzakeyo.
si latet fur, dominus domus applicabitur ad deos, et jurabit quod non extenderit manum in rem proximi sui,
9 Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri.
ad perpetrandam fraudem, tam in bove quam in asino, et ove ac vestimento, et quidquid damnum inferre potest: ad deos utriusque causa perveniet, et si illi judicaverint, duplum restituet proximo suo.
10 “Ngati munthu wina anasungitsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa, kapena chiweto chilichonse ndipo chiweto chija nʼkufa kapena kupweteka kapena kutengedwa popanda wina kuona,
Si quis commendaverit proximo suo asinum, bovem, ovem, et omne jumentum ad custodiam, et mortuum fuerit, aut debilitatum, vel captum ab hostibus, nullusque hoc viderit:
11 ndiye kuti anthu awiriwo ayenera kulumbira pamaso pa Mulungu kuti asatenge chinthu cha mnzake. Zikatero mwini katundu uja avomereze zimenezi ndipo asabwezeredwe kanthu.
jusjurandum erit in medio, quod non extenderit manum ad rem proximi sui: suscipietque dominus juramentum, et ille reddere non cogetur.
12 Koma ngati chiwetocho chinabedwa, iye ayenera kubwezera mwini wakeyo.
Quod si furto ablatum fuerit, restituet damnum domino;
13 Ngati chinagwidwa ndi zirombo, iye ayenera kubweretsa zotsalira ngati umboni ndipo sadzalipira kanthu.
si comestum a bestia, deferat ad eum quod occisum est, et non restituet.
14 “Ngati munthu abwereka chiweto cha mnzake ndipo chiweto chija nʼkuvulala kapena kufa chikanali ndi iyebe, wobwerekayo ayenera kulipira.
Qui a proximo suo quidquam horum mutuo postulaverit, et debilitatum aut mortuum fuerit domino non præsente, reddere compelletur.
15 Koma ngati mwini wakeyo ali ndi chiwetocho, wobwerekayo sadzalipira. Ngati anapereka ndalama pobwereka chiwetocho, ndalama anaperekazo zilowa mʼmalo mwa chiweto chakufacho.
Quod si impræsentiarum dominus fuerit, non restituet, maxime si conductum venerat pro mercede operis sui.
16 “Ngati munthu anyenga namwali wosadziwa mwamuna amene sanapalidwe ubwenzi ndi kugona naye, munthuyo ayenera kulipira malowolo ndipo adzakhala mkazi wake.
Si seduxerit quis virginem necdum desponsatam, dormieritque cum ea: dotabit eam, et habebit eam uxorem.
17 Ngati abambo ake akanitsitsa kwamtuwagalu kumupereka kuti amukwatire, munthuyo aperekebe malowolo woyenera namwaliyo.
Si pater virginis dare noluerit, reddet pecuniam juxta modum dotis, quam virgines accipere consueverunt.
18 “Musayilole mfiti yayikazi kuti ikhale ndi moyo.
Maleficos non patieris vivere.
19 “Aliyense wogonana ndi chiweto ayenera kuphedwa.
Qui coierit cum jumento, morte moriatur.
20 “Aliyense wopereka nsembe kwa mulungu wina osati Yehova awonongedwe.
Qui immolat diis, occidetur, præterquam Domino soli.
21 “Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto.
Advenam non contristabis, neque affliges eum: advenæ enim et ipsi fuistis in terra Ægypti.
22 “Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.
Viduæ et pupillo non nocebitis.
23 Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo.
Si læseritis eos, vociferabuntur ad me, et ego audiam clamorem eorum:
24 Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo.
et indignabitur furor meus, percutiamque vos gladio, et erunt uxores vestræ viduæ, et filii vestri pupilli.
25 “Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja.
Si pecuniam mutuam dederis populo meo pauperi qui habitat tecum, non urgebis eum quasi exactor, nec usuris opprimes.
26 Mukatenga chovala cha mnzanu kuti chikhale chikole mumubwezere dzuwa lisanalowe
Si pignus a proximo tuo acceperis vestimentum, ante solis occasum reddes ei.
27 chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo.
Ipsum enim est solum, quo operitur, indumentum carnis ejus, nec habet aliud in quo dormiat: si clamaverit ad me, exaudiam eum, quia misericors sum.
28 “Musachite chipongwe Mulungu wanu kapena kutemberera mtsogoleri wa anthu anu.
Diis non detrahes, et principi populi tui non maledices.
29 “Musachedwe kupereka kwa Ine zokolola zanu zochuluka ndi vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna.
Decimas tuas et primitias tuas non tardabis reddere: primogenitum filiorum tuorum dabis mihi.
30 Muchite chimodzimodzi ndi ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwa azikhala ndi amayi ake masiku asanu ndi awiri. Koma pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo muzimupereka kwa Ine.
De bobus quoque, et ovibus similiter facies: septem diebus sit cum matre sua, die octava reddes illum mihi.
31 “Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.”
Viri sancti eritis mihi: carnem, quæ a bestiis fuerit prægustata, non comedetis, sed projicietis canibus.

< Eksodo 22 >