< 2 Samueli 7 >

1 Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira,
It happened, when the king lived in his house, and YHWH had given him rest from all his enemies all around,
2 mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.”
that the king said to Nathan the prophet, "See now, I dwell in a house of cedar, but the ark of God dwells within curtains."
3 Natani anayankha mfumu kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu chifukwa Yehova ali nanu.”
Nathan said to the king, "Go, do all that is in your heart; for YHWH is with you."
4 Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati,
It happened the same night, that the word of YHWH came to Nathan, saying,
5 “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo?
"Go and tell my servant David, 'Thus says YHWH, "Shall you build me a house for me to dwell in?
6 Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti.
For I have not lived in a house since the day that I brought up the children of Israel out of Egypt, even to this day, but have moved around in a tent and in a tabernacle.
7 Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense atsogoleri awo, amene ndinamulamula kuweta anthu anga Aisraeli kuti, nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”
In all places in which I have walked throughout Israel, did I say a word to any of the judges of Israel, whom I commanded to be shepherd of my people Israel, saying, 'Why have you not built me a house of cedar?'"'
8 “Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli.
Now therefore you shall tell my servant David this, 'Thus says YHWH of hosts, "I took you from the sheep pen, from following the sheep, that you should be prince over my people Israel.
9 Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.
I have been with you wherever you went, and have cut off all your enemies from before you. I will make you a great name, like the name of the great ones who are in the earth.
10 Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja,
I will appoint a place for my people Israel, and will plant them, that they may dwell in their own place, and be moved no more; neither shall the children of wickedness afflict them any more, as at the first,
11 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse. “‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako:
and from the time that I commanded judges to be over my people Israel. I will cause you to rest from all your enemies. Moreover YHWH tells you that he will build you a house.
12 Masiku ako akadzatha ndipo ukadzakapuma ndi makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, imene idzachokera mʼthupi mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.
And it will come about when your days are fulfilled, and you sleep with your fathers, that I will raise up your descendant after you, who will come from your body, and I will establish his kingdom.
13 Iye ndiye amene adzamangire nyumba Dzina langa, ndipo Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya.
He will build a house for my name, and I will establish his throne forever.
14 Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu.
I will be his father, and he shall be my son. If he commits iniquity, I will chasten him with a human rod, and with the stripes from human beings;
15 Koma sindidzasiya kumukonda, monga ndinachitira ndi Sauli, amene ndinamuchotsa iwe usanakhale mfumu.
but my loving kindness I will not take from him, as I took it from Saul, whom I put away before you.
16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’”
And your house and your kingdom shall be made sure forever before me, and your throne shall be established forever."'"
17 Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.
According to all these words, and according to all this vision, so Nathan spoke to David.
18 Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati: “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?”
Then king David went in and sat before YHWH and said, "Who am I, Lord YHWH, and what is my house, that you have brought me thus far?
19 Ndipo kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Kodi umu ndi mmene mumachitira ndi munthu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse?
This was a small thing in your eyes, Lord YHWH, and you have spoken of your servant's house for a great while to come, and you have let me look upon the generation of humankind to come, Lord YHWH.
20 Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu? Pakuti Inu Ambuye Wamphamvuzonse mukumudziwa mtumiki wanu.
And what more can David add to you concerning the honor which is done to your servant? For you know your servant, YHWH.
21 Chifukwa cha mawu anu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwachiwulula kwa mtumiki wanu.
For your servant's sake, and according to your own heart, you have worked all this greatness, to make your servant know it.
22 Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu.
Therefore you are great, Lord YHWH. For there is none like you, neither is there any God besides you, according to all that we have heard with our ears.
23 Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto?
And who is like your people Israel, the one nation on earth whom God went out to redeem to be a people for himself, and to make a name for yourself, and to do great and awesome deeds by driving out before your people, whom you redeemed for yourself from Egypt, a nation and its gods?
24 Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.
And you established your people Israel for yourself to be your people forever; and you, YHWH, became their God.
25 “Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera,
Now, Lord YHWH, the word that you have spoken concerning your servant, and concerning his house, confirm it forever, and do as you have spoken.
26 kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
Let your name be magnified forever, saying, 'YHWH of hosts is the God of Israel,' and the house of your servant David shall be established before you.
27 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere.
For you have revealed to your servant, saying, 'I will build you a house.' Therefore your servant has found in his heart to pray this prayer to you.
28 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu.
"Now, O Lord YHWH, you are God, and your words are truth, and you have promised this good thing to your servant.
29 Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”
Now therefore let it please you to bless the house of your servant, that it may continue forever before you; for you, Lord YHWH, have spoken it. Let the house of your servant be blessed forever with your blessing."

< 2 Samueli 7 >