< 1 Atesalonika 5 >

1 Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni,
О временах же и сроках нет нужды писать к вам, братия,
2 chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku.
ибо сами вы достоверно знаете, что день Господень так придет, как тать ночью.
3 Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.
Ибо, когда будут говорить: “мир и безопасность”, тогда внезапно постигнет их пагуба, подобно как мука родами постигает имеющую во чреве, и не избегнут.
4 Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala.
Но вы, братия, не во тьме, чтобы день застал вас, как тать.
5 Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima.
Ибо все вы - сыны света и сыны дня: мы - не сыны ночи, ни тьмы.
6 Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga.
Итак, не будем спать, как и прочие, но будем бодрствовать и трезвиться.
7 Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku.
Ибо спящие спят ночью, и упивающиеся упиваются ночью.
8 Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa.
Мы же, будучи сынами дня, да трезвимся, облекшись в броню веры и любви и в шлем надежды спасения,
9 Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
потому что Бог определил нас не на гнев, но к получению спасения через Господа нашего Иисуса Христа,
10 Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi.
умершего за нас, чтобы мы бодрствуем ли, или спим, жили вместе с Ним.
11 Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
Посему увещевайте друг друга и назидайте один другого, как вы и делаете.
12 Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani.
Просим же вас, братия, уважать трудящихся у вас, и предстоятелей ваших в Господе, и вразумляющих вас,
13 Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.
и почитать их преимущественно с любовью за дело их; будьте в мире между собою.
14 Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense.
Умоляем также вас, братия, вразумляйте бесчинных, утешайте малодушных, поддерживайте слабых, будьте долготерпеливы ко всем.
15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
Смотрите, чтобы кто кому не воздавал злом за зло; но всегда ищите добра и друг другу и всем.
16 Kondwerani nthawi zonse.
Всегда радуйтесь.
17 Pempherani kosalekeza.
Непрестанно молитесь.
18 Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
За все благодарите: ибо такова о вас воля Божия во Христе Иисусе.
19 Musazimitse moto wa Mzimu Woyera.
Духа не угашайте.
20 Musanyoze mawu a uneneri.
Пророчества не уничижайте.
21 Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino.
Все испытывайте, хорошего держитесь.
22 Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.
Удерживайтесь от всякого рода зла.
23 Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Сам же Бог мира да освятит вас во всей полноте, и ваш дух, и душа, и тело во всей целости да сохранится без порока в пришествие Господа нашего Иисуса Христа.
24 Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.
Верен Призывающий вас, Который и сотворит сие.
25 Abale, mutipempherere.
Братия! молитесь о нас.
26 Perekani moni wachikondi kwa onse.
Приветствуйте всех братьев лобзанием святым.
27 Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.
Заклинаю вас Господом прочитать сие послание всем святым братиям.
28 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.
Благодать Господа нашего Иисуса Христа с вами. Аминь.

< 1 Atesalonika 5 >