< 1 Akorinto 1 >

1 Paulo, woyitanidwa mwachifuniro cha Mulungu kuti akhale mtumwi wa Khristu Yesu ndi mʼbale wathu Sositene.
Paul, called [to be] an apostle of Jesus Christ through the will of God, and Sosthenes [our] brother,
2 Kupita ku mpingo wa Mulungu ku Korinto, kwa oyeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi oyitanidwa kukhala opatulika ndiponso kwa onse amene amapemphera mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu mʼdziko lonse lapansi, amene ndi Ambuye wawo ndi wathunso.
To the church of God which is at Corinth, to them that are sanctified in Christ Jesus, called [to be] saints, with all that in every place call upon the name of Jesus Christ our Lord, both theirs and ours.
3 Landirani chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu.
Grace [be] to you, and peace from God our Father, and [from] the Lord Jesus Christ.
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu.
I thank my God always on your behalf, for the grace of God which is given you by Jesus Christ;
5 Pakuti mwa Iye mwalemekezedwa mʼnjira iliyonse, mʼkuyankhula kwanu konse ndi mʼkudziwa kwanu konse,
That in every thing ye are enriched by him, in all utterance, and [in] all knowledge;
6 chifukwa umboni wathu pa za Khristu unatsimikizidwa mwa inu.
Even as the testimony of Christ was confirmed in you:
7 Choncho inu simusowa mphatso yauzimu iliyonse pamene mukudikira mofunitsitsa kuti Ambuye athu Yesu Khristu avumbulutsidwe.
So that ye come behind in no gift; waiting for the coming of our Lord Jesus Christ:
8 Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Who will also confirm you to the end, [that ye may be] blameless in the day of our Lord Jesus Christ.
9 Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.
God [is] faithful, by whom ye were called to the fellowship of his Son Jesus Christ our Lord.
10 Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo.
Now I beseech you, brethren, by the name of our Lord Jesus Christ, that ye all speak the same thing, and [that] there be no divisions among you; but [that] ye be perfectly joined together in the same mind, and in the same judgment.
11 Abale anga, ena a ku nyumba ya Kloe andidziwitsa kuti pali mkangano pakati panu.
For it hath been declared to me concerning you, my brethren, by them [who are of the house] of Chloe, that there are contentions among you.
12 Chimene ndikutanthauza ndi ichi: wina amati, “Ndimatsatira Paulo,” wina, “Ndimatsatira Apolo,” wina, “Ndimatsatira Kefa,” winanso, “Ndimatsatira Khristu.”
Now this I say, that every one of you saith, I am of Paul; and I of Apollos; and I of Cephas; and I of Christ.
13 Kodi Khristu wagawikana? Kodi Paulo anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha inu? Kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo?
Is Christ divided? was Paul crucified for you? or were ye baptized in the name of Paul?
14 Ine ndikuyamika kuti sindinabatizepo mmodzi mwa inu kupatula Krispo ndi Gayo,
I thank God that I baptized none of you, but Crispus and Gaius;
15 mwakuti palibe amene anganene kuti anabatizidwa mʼdzina langa.
Lest any should say that I had baptized in my own name.
16 (Inde, ine ndinabatizanso a mʼbanja la Stefano, koma sindikumbukira ngati ndinabatizanso wina aliyense).
And I baptized also the household of Stephanas; besides, I know not whether I baptized any other.
17 Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.
For Christ hath not sent me to baptize, but to preach the gospel: not with wisdom of words, lest the cross of Christ should be made of no effect.
18 Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu.
For the preaching of the cross is to them that perish, foolishness; but to us who are saved, it is the power of God.
19 Pakuti kwalembedwa kuti, “Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru; luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
For it is written, I will destroy the wisdom of the wise, and will bring to nothing the understanding of the prudent.
20 Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi? (aiōn g165)
Where [is] the wise? where [is] the scribe? where [is] the disputer of this world? hath not God made foolish the wisdom of this world? (aiōn g165)
21 Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira.
For when in the wisdom of God the world by wisdom knew not God, it pleased God by the foolishness of preaching to save them that believe.
22 Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru,
For the Jews require a sign, and the Greeks seek wisdom:
23 koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina.
But we preach Christ crucified, to the Jews a stumbling-block, and to the Greeks foolishness;
24 Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu.
But to them who are called, both Jews and Greeks, Christ the power of God, and the wisdom of God.
25 Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
Because the foolishness of God is wiser than men; and the weakness of God is stronger than men.
26 Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero.
For ye see your calling, brethren, that not many wise men after the flesh, not many mighty, not many noble [are called]:
27 Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu.
But God hath chosen the foolish things of the world to confound the wise; and God hath chosen the weak things of the world to confound the things which are mighty;
28 Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo,
And base things of the world, and things which are despised, hath God chosen, and things which are not, to bring to naught things that are:
29 kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu.
That no flesh should glory in his presence.
30 Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.
But of him are ye in Christ Jesus, who from God is made to us wisdom, and righteousness, and sanctification, and redemption:
31 Choncho poti zinalembedwa kuti, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
That, according as it is written, He that glorieth, let him glory in the Lord.

< 1 Akorinto 1 >