< پیدایش 5 >

این است کتاب پیدایش آدم. در روزی که خدا آدم را آفرید، به شبیه خدا او راساخت. ۱ 1
Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.
نر و ماده ایشان را آفرید. و ایشان رابرکت داد و ایشان را «آدم» نام نهاد، در روزآفرینش ایشان. ۲ 2
Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
و آدم صد و سی سال بزیست، پس پسری به شبیه و بصورت خود آورد، و او را شیث نامید. ۳ 3
Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
وایام آدم بعد از آوردن شیث، هشتصد سال بود، وپسران و دختران آورد. ۴ 4
Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
پس تمام ایام آدم که زیست، نهصد و سی سال بود که مرد. ۵ 5
Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
و شیث صد و پنج سال بزیست، و انوش را آورد. ۶ 6
Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.
وشیث بعد از آوردن انوش، هشتصد و هفت سال بزیست و پسران و دختران آورد. ۷ 7
Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
و جمله ایام شیث، نهصد و دوازده سال بود که مرد. ۸ 8
Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
و انوش نود سال بزیست، و قینان را آورد. ۹ 9
Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani.
و انوش بعداز آوردن قینان، هشتصد و پانزده سال زندگانی کرد و پسران و دختران آورد. ۱۰ 10
Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
پس جمله ایام انوش نهصد و پنج سال بود که مرد. ۱۱ 11
Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
و قینان هفتاد سال بزیست، و مهللئیل را آورد. ۱۲ 12
Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli.
و قینان بعد از آوردن مهللئیل، هشتصد و چهل سال زندگانی کرد و پسران و دختران آورد. ۱۳ 13
Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
و تمامی ایام قینان، نهصد و ده سال بود که مرد. ۱۴ 14
Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
ومهللئیل، شصت و پنج سال بزیست، و یارد را آورد. ۱۵ 15
Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.
و مهللئیل بعد از آوردن یارد، هشتصد وسی سال زندگانی کرد و پسران و دختران آورد. ۱۶ 16
Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
پس همه ایام مهللئیل، هشتصد و نود و پنج سال بود که مرد. ۱۷ 17
Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.
و یارد صد و شصت و دو سال بزیست، و خنوخ را آورد. ۱۸ 18
Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki.
و یارد بعد از آوردن خنوخ، هشتصد سال زندگانی کرد و پسران ودختران آورد. ۱۹ 19
Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
و تمامی ایام یارد، نهصد وشصت و دو سال بود که مرد. ۲۰ 20
Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.
و خنوخ شصت وپنج سال بزیست، و متوشالح را آورد. ۲۱ 21
Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela.
و خنوخ بعد از آوردن متوشالح، سیصد سال با خدا راه می‌رفت و پسران و دختران آورد. ۲۲ 22
Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
و همه ایام خنوخ، سیصد و شصت و پنج سال بود. ۲۳ 23
Zaka zonse za Enoki zinali 365.
وخنوخ با خدا راه می‌رفت و نایاب شد، زیرا خدااو را برگرفت. ۲۴ 24
Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
و متوشالح صد و هشتاد و هفت سال بزیست، و لمک را آورد. ۲۵ 25
Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki.
و متوشالح بعداز آوردن لمک، هفتصد و هشتاد و دو سال زندگانی کرد و پسران و دختران آورد. ۲۶ 26
Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
پس جمله ایام متوشالح، نهصد و شصت و نه سال بودکه مرد. ۲۷ 27
Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
و لمک صد و هشتاد و دو سال بزیست، و پسری آورد. ۲۸ 28
Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna.
و وی را نوح نام نهاده گفت: «این ما را تسلی خواهد داد از اعمال ما و ازمحنت دستهای ما از زمینی که خداوند آن راملعون کرد.» ۲۹ 29
Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”
و لمک بعد از آوردن نوح، پانصدو نود و پنج سال زندگانی کرد و پسران و دختران آورد. ۳۰ 30
Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
پس تمام ایام لمک، هفتصد و هفتاد وهفت سال بود که مرد. ۳۱ 31
Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
و نوح پانصد ساله بود، پس نوح سام و حام و یافث را آورد. ۳۲ 32
Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.

< پیدایش 5 >