< Romans 10 >

1 Brothers, my heart’s desire and my prayer to God is for Israel, that they may be saved.
Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.
2 For I testify about them that they have a zeal for God, but not according to knowledge.
Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.
3 For being ignorant of God’s righteousness, and seeking to establish their own righteousness, they didn’t subject themselves to the righteousness of God.
Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu.
4 For Christ is the fulfillment of the law for righteousness to everyone who believes.
Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.
5 For Moses writes about the righteousness of the law, “The one who does them will live by them.”
Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
6 But the righteousness which is of faith says this, “Don’t say in your heart, ‘Who will ascend into heaven?’ (that is, to bring Christ down);
Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’” (ndiko, kukatsitsa Khristu)
7 or, ‘Who will descend into the abyss?’ (that is, to bring Christ up from the dead.)” (Abyssos g12)
“kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa). (Abyssos g12)
8 But what does it say? “The word is near you, in your mouth and in your heart;” that is, the word of faith which we preach:
Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira,
9 that if you will confess with your mouth that Jesus is Lord and believe in your heart that God raised him from the dead, you will be saved.
kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
10 For with the heart one believes resulting in righteousness; and with the mouth confession is made resulting in salvation.
Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.
11 For the Scripture says, “Whoever believes in him will not be disappointed.”
Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”
12 For there is no distinction between Jew and Greek; for the same Lord is Lord of all, and is rich to all who call on him.
Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye
13 For, “Whoever will call on the name of the Lord will be saved.”
pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
14 How then will they call on him in whom they have not believed? How will they believe in him whom they have not heard? How will they hear without a preacher?
Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?
15 And how will they preach unless they are sent? As it is written: “How beautiful are the feet of those who preach the Good News of peace, who bring glad tidings of good things!”
Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”
16 But they didn’t all listen to the glad news. For Isaiah says, “Lord, who has believed our report?”
Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?”
17 So faith comes by hearing, and hearing by the word of God.
Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.
18 But I say, didn’t they hear? Yes, most certainly, “Their sound went out into all the earth, their words to the ends of the world.”
Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
19 But I ask, didn’t Israel know? First Moses says, “I will provoke you to jealousy with that which is no nation. I will make you angry with a nation void of understanding.”
Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti, “Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake. Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
20 Isaiah is very bold and says, “I was found by those who didn’t seek me. I was revealed to those who didn’t ask for me.”
Ndipo Yesaya molimba mtima akuti, “Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”
21 But about Israel he says, “All day long I stretched out my hands to a disobedient and contrary people.”
Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti, “Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga kwa anthu osandimvera ndi okanika.”

< Romans 10 >