< Philippians 2 >

1 If therefore there is any exhortation in Christ, if any consolation of love, if any fellowship of the Spirit, if any tender mercies and compassion,
Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo,
2 make my joy full by being like-minded, having the same love, being of one accord, of one mind;
tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso.
3 doing nothing through rivalry or through conceit, but in humility, each counting others better than himself;
Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.
4 each of you not just looking to his own things, but each of you also to the things of others.
Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
5 Have this in your mind, which was also in Christ Jesus,
Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:
6 who, existing in the form of God, didn’t consider equality with God a thing to be grasped,
Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
7 but emptied himself, taking the form of a servant, being made in the likeness of men.
Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
8 And being found in human form, he humbled himself, becoming obedient to the point of death, yes, the death of the cross.
Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!
9 Therefore God also highly exalted him, and gave to him the name which is above every name,
Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 that at the name of Jesus every knee should bow, of those in heaven, those on earth, and those under the earth,
kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 and that every tongue should confess that Jesus Christ is Lord, to the glory of God the Father.
ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.
12 So then, my beloved, even as you have always obeyed, not only in my presence, but now much more in my absence, work out your own salvation with fear and trembling.
Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera,
13 For it is God who works in you both to will and to work for his good pleasure.
pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.
14 Do all things without complaining and arguing,
Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo,
15 that you may become blameless and harmless, children of God without defect in the middle of a crooked and perverse generation, among whom you are seen as lights in the world,
kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba
16 holding up the word of life, that I may have something to boast in the day of Christ that I didn’t run in vain nor labor in vain.
powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe.
17 Yes, and if I am poured out on the sacrifice and service of your faith, I am glad and rejoice with you all.
Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse.
18 In the same way, you also should be glad and rejoice with me.
Chomwechonso, inu khalani okondwa ndi osangalala nane pamodzi.
19 But I hope in the Lord Jesus to send Timothy to you soon, that I also may be cheered up when I know how you are doing.
Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko, kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu.
20 For I have no one else like-minded, who will truly care about you.
Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu.
21 For they all seek their own, not the things of Jesus Christ.
Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu.
22 But you know that he has proved himself. As a child serves a father, so he served with me in furtherance of the Good News.
Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake.
23 Therefore I hope to send him at once, as soon as I see how it will go with me.
Choncho ndikuyembekezera kumutuma msanga ndikangodziwa mmene zinthu zanga ziyendere.
24 But I trust in the Lord that I myself also will come shortly.
Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa.
25 But I thought it necessary to send to you Epaphroditus, my brother, fellow worker, fellow soldier, and your apostle and servant of my need,
Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga.
26 since he longed for you all, and was very troubled because you had heard that he was sick.
Pakuti akukulakalakani nonsenu ndipo akusauka mu mtima chifukwa munamva kuti akudwala.
27 For indeed he was sick nearly to death, but God had mercy on him, and not on him only, but on me also, that I might not have sorrow on sorrow.
Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke.
28 I have sent him therefore the more diligently, that when you see him again, you may rejoice, and that I may be the less sorrowful.
Choncho khumbo langa lofulumiza kumutumiza lakula, kuti pamene mumuonenso musangalale komanso kuti nkhawa yanga ichepe.
29 Receive him therefore in the Lord with all joy, and hold such people in honor,
Mulandireni mwa Ambuye ndi chimwemwe chachikulu, ndipo anthu onga iyeyu muziwachitira ulemu.
30 because for the work of Christ he came near to death, risking his life to supply that which was lacking in your service toward me.
Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.

< Philippians 2 >