< Philemon 1 >

1 Paul, a prisoner of Christ Jesus, and Timothy our brother, to Philemon, our beloved fellow worker,
Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu. Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu.
2 to the beloved Apphia, to Archippus our fellow soldier, and to the assembly in your house:
Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu.
3 Grace to you and peace from God our Father and the Lord Jesus Christ.
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
4 I thank my God always, making mention of you in my prayers,
Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga.
5 hearing of your love and of the faith which you have toward the Lord Jesus and toward all the saints,
Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse.
6 that the fellowship of your faith may become effective in the knowledge of every good thing which is in us in Christ Jesus.
Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu.
7 For we have much joy and comfort in your love, because the hearts of the saints have been refreshed through you, brother.
Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye.
8 Therefore though I have all boldness in Christ to command you that which is appropriate,
Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita,
9 yet for love’s sake I rather appeal to you, being such a one as Paul, the aged, but also a prisoner of Jesus Christ.
komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu,
10 I appeal to you for my child Onesimus, whom I have become the father of in my chains,
ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo.
11 who once was useless to you, but now is useful to you and to me.
Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso.
12 I am sending him back. Therefore receive him, that is, my own heart,
Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni.
13 whom I desired to keep with me, that on your behalf he might serve me in my chains for the Good News.
Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino.
14 But I was willing to do nothing without your consent, that your goodness would not be as of necessity, but of free will.
Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza.
15 For perhaps he was therefore separated from you for a while that you would have him forever, (aiōnios g166)
Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. (aiōnios g166)
16 no longer as a slave, but more than a slave, a beloved brother—especially to me, but how much rather to you, both in the flesh and in the Lord.
Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.
17 If then you count me a partner, receive him as you would receive me.
Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo.
18 But if he has wronged you at all or owes you anything, put that to my account.
Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo.
19 I, Paul, write this with my own hand: I will repay it (not to mention to you that you owe to me even your own self besides).
Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo.
20 Yes, brother, let me have joy from you in the Lord. Refresh my heart in the Lord.
Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu.
21 Having confidence in your obedience, I write to you, knowing that you will do even beyond what I say.
Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.
22 Also, prepare a guest room for me, for I hope that through your prayers I will be restored to you.
Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.
23 Epaphras, my fellow prisoner in Christ Jesus, greets you,
Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni.
24 as do Mark, Aristarchus, Demas, and Luke, my fellow workers.
Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.
25 The grace of our Lord Jesus Christ be with your spirit. Amen.
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.

< Philemon 1 >