< 2 Corinthians 1 >

1 Paul, an apostle of Christ Jesus through the will of God, and Timothy our brother, to the assembly of God which is at Corinth, with all the saints who are in the whole of Achaia:
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo, Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse.
2 Grace to you and peace from God our Father and the Lord Jesus Christ.
Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
3 Blessed be the God and Father of our Lord Jesus Christ, the Father of mercies and God of all comfort,
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse.
4 who comforts us in all our affliction, that we may be able to comfort those who are in any affliction, through the comfort with which we ourselves are comforted by God.
Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.
5 For as the sufferings of Christ abound to us, even so our comfort also abounds through Christ.
Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri.
6 But if we are afflicted, it is for your comfort and salvation. If we are comforted, it is for your comfort, which produces in you the patient enduring of the same sufferings which we also suffer.
Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife.
7 Our hope for you is steadfast, knowing that, since you are partakers of the sufferings, so you are also of the comfort.
Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.
8 For we do not desire to have you uninformed, brothers, concerning our affliction which happened to us in Asia: that we were weighed down exceedingly, beyond our power, so much that we despaired even of life.
Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo.
9 Yes, we ourselves have had the sentence of death within ourselves, that we should not trust in ourselves, but in God who raises the dead,
Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa.
10 who delivered us out of so great a death, and does deliver, on whom we have set our hope that he will also still deliver us,
Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe.
11 you also helping together on our behalf by your supplication; that, for the gift given to us by means of many, thanks may be given by many persons on your behalf.
Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri.
12 For our boasting is this: the testimony of our conscience that in holiness and sincerity of God, not in fleshly wisdom but in the grace of God, we behaved ourselves in the world, and more abundantly toward you.
Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu.
13 For we write no other things to you than what you read or even acknowledge, and I hope you will acknowledge to the end—
Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa.
14 as also you acknowledged us in part—that we are your boasting, even as you also are ours, in the day of our Lord Jesus.
Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu.
15 In this confidence, I was determined to come first to you, that you might have a second benefit,
Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri.
16 and by you to pass into Macedonia, and again from Macedonia to come to you, and to be sent forward by you on my journey to Judea.
Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya.
17 When I therefore planned this, did I show fickleness? Or the things that I plan, do I plan according to the flesh, that with me there should be the “Yes, yes” and the “No, no?”
Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
18 But as God is faithful, our word toward you was not “Yes and no.”
Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.”
19 For the Son of God, Jesus Christ, who was preached among you by us—by me, Silvanus, and Timothy—was not “Yes and no,” but in him is “Yes.”
Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.”
20 For however many are the promises of God, in him is the “Yes.” Therefore also through him is the “Amen”, to the glory of God through us.
Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu.
21 Now he who establishes us with you in Christ and anointed us is God,
Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife,
22 who also sealed us and gave us the down payment of the Spirit in our hearts.
nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.
23 But I call God for a witness to my soul, that to spare you, I did not come to Corinth.
Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni.
24 We do not control your faith, but are fellow workers with you for your joy. For you stand firm in faith.
Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.

< 2 Corinthians 1 >