< 1 John 3 >

1 See how great a love the Father has given to us, that we should be called children of God! For this cause the world does not know us, because it did not know him.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
2 Beloved, now we are children of God. It is not yet revealed what we will be; but we know that when he is revealed, we will be like him, for we will see him just as he is.
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.
3 Everyone who has this hope set on him purifies himself, even as he is pure.
Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.
4 Everyone who sins also commits lawlessness. Sin is lawlessness.
Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo.
5 You know that he was revealed to take away our sins, and no sin is in him.
Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo.
6 Whoever remains in him does not sin. Whoever sins has not seen him and does not know him.
Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.
7 Little children, let no one lead you astray. He who does righteousness is righteous, even as he is righteous.
Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama.
8 He who sins is of the devil, for the devil has been sinning from the beginning. To this end the Son of God was revealed: that he might destroy the works of the devil.
Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi.
9 Whoever is born of God does not commit sin, because his seed remains in him, and he cannot sin, because he is born of God.
Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.
10 In this the children of God are revealed, and the children of the devil. Whoever does not do righteousness is not of God, neither is he who does not love his brother.
Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.
11 For this is the message which you heard from the beginning, that we should love one another—
Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake.
12 unlike Cain, who was of the evil one and killed his brother. Why did he kill him? Because his deeds were evil, and his brother’s righteous.
Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama.
13 Do not be surprised, my brothers, if the world hates you.
Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu.
14 We know that we have passed out of death into life, because we love the brothers. He who does not love his brother remains in death.
Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa.
15 Whoever hates his brother is a murderer, and you know that no murderer has consummate (aiōnios g166) life remaining in him.
Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha. (aiōnios g166)
16 By this we know love, because he laid down his life for us. And we ought to lay down our lives for the brothers.
Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
17 But whoever has the world’s goods and sees his brother in need, then closes his heart of compassion against him, how does God’s love remain in him?
Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?
18 My little children, let’s not love in word only, or with the tongue only, but in deed and truth.
Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.
19 And by this we know that we are of the truth and persuade our hearts before him,
Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu,
20 because if our heart condemns us, God is greater than our heart, and knows all things.
nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.
21 Beloved, if our hearts do not condemn us, we have boldness toward God;
Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu.
22 so whatever we ask, we receive from him, because we keep his commandments and do the things that are pleasing in his sight.
Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa.
23 This is his commandment, that we should believe in the name of his Son, Jesus Christ, and love one another, even as he commanded.
Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira.
24 He who keeps his commandments remains in him, and he in him. By this we know that he remains in us, by the Spirit which he gave us.
Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.

< 1 John 3 >