< 马太福音 12 >

1 那时,耶稣在安息日从麦地经过。他的门徒饿了,就掐起麦穗来吃。
Pa nthawi imeneyo Yesu anadutsa pakati pa minda ya tirigu pa tsiku la Sabata. Ophunzira ake anamva njala nayamba kuthyola ngala za tirigu nʼkumadya.
2 法利赛人看见,就对耶稣说:“看哪,你的门徒做安息日不可做的事了!”
Afarisi ataona zimenezi anati kwa Iye, “Taonani! Ophunzira anu akuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata.”
3 耶稣对他们说:“经上记着大卫和跟从他的人饥饿之时所做的事,你们没有念过吗?
Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene anachita Davide pamene iye ndi anzake anamva njala?
4 他怎么进了 神的殿,吃了陈设饼,这饼不是他和跟从他的人可以吃得,惟独祭司才可以吃。
Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha.
5 再者,律法上所记的,当安息日,祭司在殿里犯了安息日还是没有罪,你们没有念过吗?
Kodi simunawerenge mʼmalamulo kuti pa Sabata ansembe mʼNyumba ya Mulungu amaphwanya lamulo la Sabata komabe sawayesa olakwa?
6 但我告诉你们,在这里有一人比殿更大。
Ine ndikuwuzani kuti wamkulu kuposa Nyumba ya Mulunguyo ali pano.
7 ‘我喜爱怜恤,不喜爱祭祀。’你们若明白这话的意思,就不将无罪的当作有罪的了。
Ngati mukanadziwa zomwe mawu awa atanthauza, ‘Ine ndifuna chifundo osati nsembe,’ inu simukanatsutsa osalakwa.
8 因为人子是安息日的主。”
Pakuti Mwana wa Munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”
9 耶稣离开那地方,进了一个会堂。
Atachoka kumeneko anakalowa mʼsunagoge mwawo.
10 那里有一个人枯干了一只手。有人问耶稣说:“安息日治病可以不可以?”意思是要控告他。
Ndipo mʼmenemo munali munthu wolumala dzanja. Pofuna chifukwa chokamunenezera, iwo anamufunsa Yesu kuti, “Kodi nʼkololedwa kuchiritsa munthu tsiku la Sabata?”
11 耶稣说:“你们中间谁有一只羊,当安息日掉在坑里,不把它抓住、拉上来呢?
Iye anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu ali ndi nkhosa nigwera mʼdzenje tsiku la Sabata, kodi simudzayigwira ndi kuyitulutsa kunja?
12 人比羊何等贵重呢!所以,在安息日做善事是可以的。”
Nanga munthu sali oposa nkhosa kwambiri! Chifukwa chake nʼkololedwa kuchita zabwino pa Sabata.”
13 于是对那人说:“伸出手来!”他把手一伸,手就复了原,和那只手一样。
Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale.
14 法利赛人出去,商议怎样可以除灭耶稣。
Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere.
15 耶稣知道了,就离开那里,有许多人跟着他。他把其中有病的人都治好了;
Podziwa zimenezi, Yesu anachoka kumalo amenewo. Ambiri anamutsata Iye ndipo anachiritsira odwala awo onse
16 又嘱咐他们,不要给他传名。
nawachenjeza kuti asamuwulule kuti yani.
17 这是要应验先知以赛亚的话,说:
Uku kunali kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
18 看哪!我的仆人, 我所拣选、所亲爱、心里所喜悦的, 我要将我的灵赐给他; 他必将公理传给外邦。
“Taonani mnyamata wanga amene ndinamusankha, Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye. Pa Iye ndidzayika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.
19 他不争竞,不喧嚷; 街上也没有人听见他的声音。
Sadzalimbana, sadzafuwula, ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake mʼmakwalala.
20 压伤的芦苇,他不折断; 将残的灯火,他不吹灭; 等他施行公理,叫公理得胜。
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyale yofuka sadzayizimitsa, kufikira Iye adzatumiza chiweruziro chikagonjetse.
21 外邦人都要仰望他的名。
Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.”
22 当下,有人将一个被鬼附着、又瞎又哑的人带到耶稣那里,耶稣就医治他,甚至那哑巴又能说话,又能看见。
Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona.
23 众人都惊奇,说:“这不是大卫的子孙吗?”
Anthu onse anadabwa ndipo anati, “Kodi uyu ndi kukhala mwana wa Davide?”
24 但法利赛人听见,就说:“这个人赶鬼,无非是靠着鬼王别西卜啊。”
Koma Afarisi atamva zimenezi, anati, “Uyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mkulu wa ziwandazo.”
25 耶稣知道他们的意念,就对他们说:“凡一国自相纷争,就成为荒场;一城一家自相纷争,必站立不住;
Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse ukagawanika mwa iwo udzawonongeka ndi mzinda uliwonse kapena banja likagawanika, mwa izo zokha sizidzayima.
26 若撒但赶逐撒但,就是自相纷争,他的国怎能站得住呢?
Ngati Satana atulutsa Satana, iye adzigawa yekha. Nanga ufumu wake ungayime bwanji?
27 我若靠着别西卜赶鬼,你们的子弟赶鬼又靠着谁呢?这样,他们就要断定你们的是非。
Ndipo ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi Belezebule, anthu anu amatulutsa ziwandazo ndi chiyani? Potero tsono adzakhala oweruza anu.
28 我若靠着 神的灵赶鬼,这就是 神的国临到你们了。
Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.
29 人怎能进壮士家里,抢夺他的家具呢?除非先捆住那壮士,才可以抢夺他的家财。
“Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.
30 不与我相合的,就是敌我的;不同我收聚的,就是分散的。”
“Iye amene sali ndi Ine atsutsana nane ndipo iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amamwaza.
31 所以我告诉你们:“人一切的罪和亵渎的话都可得赦免,惟独亵渎圣灵,总不得赦免。
Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa.
32 凡说话干犯人子的,还可得赦免;惟独说话干犯圣灵的,今世来世总不得赦免。” (aiōn g165)
Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo. (aiōn g165)
33 “你们或以为树好,果子也好;树坏,果子也坏;因为看果子就可以知道树。
“Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino ndipo mtengo woyipa umabalanso zipatso zoyipa, pajatu mtengo umadziwika ndi zipatso zake.
34 毒蛇的种类!你们既是恶人,怎能说出好话来呢?因为心里所充满的,口里就说出来。
Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima.
35 善人从他心里所存的善就发出善来;恶人从他心里所存的恶就发出恶来。
Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye.
36 我又告诉你们,凡人所说的闲话,当审判的日子,必要句句供出来;
Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula.
37 因为要凭你的话定你为义,也要凭你的话定你有罪。”
Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”
38 当时,有几个文士和法利赛人对耶稣说:“夫子,我们愿意你显个神迹给我们看。”
Pamenepo ena mwa Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anati kwa Iye, “Aphunzitsi, tikufuna tione chizindikiro chodabwitsa kuchokera kwa Inu.”
39 耶稣回答说:“一个邪恶淫乱的世代求看神迹,除了先知约拿的神迹以外,再没有神迹给他们看。
Iye anayankha kuti, “Mʼbado woyipa ndi wachigololo ufunsa za chizindikiro chodabwitsa! Koma ndi chimodzi chomwe sichidzapatsidwa kwa inu kupatula chizindikiro cha mneneri Yona.
40 约拿三日三夜在大鱼肚腹中,人子也要这样三日三夜在地里头。
Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka.
41 当审判的时候,尼尼微人要起来定这世代的罪,因为尼尼微人听了约拿所传的就悔改了。看哪,在这里有一人比约拿更大!
Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano.
42 当审判的时候,南方的女王要起来定这世代的罪;因为她从地极而来,要听所罗门的智慧话。看哪,在这里有一人比所罗门更大!”
Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.
43 “污鬼离了人身,就在无水之地过来过去,寻求安歇之处,却寻不着。
“Pamene mzimu woyipa utuluka mwa munthu, umadutsa malo wopanda madzi kufunafuna malo opumulira ndipo suwapeza.
44 于是说:‘我要回到我所出来的屋里去。’到了,就看见里面空闲,打扫干净,修饰好了,
Pamenepo umati, ‘Ndidzabwerera ku nyumba yanga komwe ndinatuluka.’ Pamene ufika, upeza mopanda kanthu, mosesedwa ndi mokonzedwa bwino.
45 便去另带了七个比自己更恶的鬼来,都进去住在那里。那人末后的景况比先前更不好了。这邪恶的世代也要如此。”
Kenaka umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa uwowo ndipo imapita ndi kukakhala mʼmenemo. Choncho khalidwe lotsiriza la munthu uyu limakhala loyipa kwambiri kuposa loyambalo. Umo ndi mmene zidzakhalire ndi mʼbado oyipawu.”
46 耶稣还对众人说话的时候,不料他母亲和他弟兄站在外边,要与他说话。
Pamene Yesu anali kuyankhulabe ndi gulu la anthu, amayi ndi abale ake anayimirira kunja, akufuna kuyankhulana naye.
47 有人告诉他说:“看哪,你母亲和你弟兄站在外边,要与你说话。”
Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunjaku akufuna kuyankhulana nanu.”
48 他却回答那人说:“谁是我的母亲?谁是我的弟兄?”
Iye anayankha kuti, “Amayi anga ndani ndipo abale anga ndi ndani?”
49 就伸手指着门徒,说:“看哪,我的母亲,我的弟兄。
Ndipo akuloza ophunzira ake, Iye anati, “Awa ndiwo amayi anga ndi abale anga.
50 凡遵行我天父旨意的人,就是我的弟兄姊妹和母亲了。”
Pakuti aliyense amene achita chifuniro cha Atate anga akumwamba ndiye mʼbale wanga, mlongo wanga ndi amayi anga.”

< 马太福音 12 >