< 历代志上 2 >

1 以色列的儿子是吕便、西缅、利未、犹大、以萨迦、西布伦、
Ana a Israeli anali awa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
2 但、约瑟、便雅悯、拿弗他利、迦得、亚设。
Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.
3 犹大的儿子是珥、俄南、示拉,这三人是迦南人书亚女儿所生的。犹大的长子珥在耶和华眼中看为恶,耶和华就使他死了。
Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha.
4 犹大的儿妇她玛给犹大生法勒斯和谢拉。犹大共有五个儿子。
Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
5 法勒斯的儿子是希斯 、哈母勒。
Ana a Perezi anali awa: Hezironi ndi Hamuli.
6 谢拉的儿子是心利、以探、希幔、甲各、大拉,共五人。
Ana a Zera anali awa: Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.
7 迦米的儿子是亚干,这亚干在当灭的物上犯了罪,连累了以色列人。
Mwana wa Karimi anali Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.
8 以探的儿子是亚撒利雅。
Mwana wa Etani anali Azariya.
9 希斯 所生的儿子是耶拉篾、兰、基路拜。
Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali: Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.
10 兰生亚米拿达;亚米拿达生拿顺。拿顺作犹大人的首领。
Ramu anabereka Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda.
11 拿顺生撒门;撒门生波阿斯;
Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi,
12 波阿斯生俄备得;俄备得生耶西;
Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.
13 耶西生长子以利押,次子亚比拿达,三子示米亚,
Yese anabereka Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea,
14 四子拿坦业,五子拉代,
wachinayi Netaneli, wachisanu Radai,
15 六子阿鲜,七子大卫。
wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide.
16 他们的姊妹是洗鲁雅和亚比该。洗鲁雅的儿子是亚比筛、约押、亚撒黑,共三人。
Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli.
17 亚比该生亚玛撒;亚玛撒的父亲是以实玛利人益帖。
Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.
18 希斯 的儿子迦勒娶阿苏巴和耶略为妻,阿苏巴的儿子是耶设、朔罢、押墩。
Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni.
19 阿苏巴死了,迦勒又娶以法她,生了户珥。
Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri.
20 户珥生乌利;乌利生比撒列。
Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.
21 希斯 正六十岁娶了基列父亲玛吉的女儿,与她同房;玛吉的女儿生了西割;
Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu.
22 西割生睚珥。睚珥在基列地有二十三个城邑。
Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi.
23 后来基述人和亚兰人夺了睚珥的城邑,并基纳和其乡村,共六十个。这都是基列父亲玛吉之子的。
(Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.
24 希斯 在迦勒·以法他死后,他的妻亚比雅给他生了亚施户;亚施户是提哥亚的父亲。
Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.
25 希斯 的长子耶拉篾生长子兰,又生布拿、阿连、阿鲜、亚希雅。
Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali: Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya.
26 耶拉篾又娶一妻名叫亚她拉,是阿南的母亲。
Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.
27 耶拉篾长子兰的儿子是玛斯、雅悯、以结。
Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa: Maazi, Yamini ndi Ekeri.
28 阿南的儿子是沙买、雅大。沙买的儿子是拿答、亚比述。
Ana a Onamu anali awa: Shamai ndi Yada. Ana a Shamai anali awa: Nadabu ndi Abisuri.
29 亚比述的妻名叫亚比孩,亚比孩给他生了亚办和摩利。
Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.
30 拿答的儿子是西列、亚遍;西列死了没有儿子。
Ana a Nadabu anali awa: Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31 亚遍的儿子是以示;以示的儿子是示珊;示珊的儿子是亚来。
Ana a Apaimu anali awa: Isi, amene anabereka Sesani. Sesani anabereka Ahilai.
32 沙买兄弟雅大的儿子是益帖、约拿单;益帖死了没有儿子。
Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa: Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.
33 约拿单的儿子是比勒、撒萨。这都是耶拉篾的子孙。
Ana a Yonatani anali awa: Peleti ndi Zaza. Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.
34 示珊没有儿子,只有女儿。示珊有一个仆人名叫耶哈,是埃及人。
Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha. Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha.
35 示珊将女儿给了仆人耶哈为妻,给他生了亚太。
Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.
36 亚太生拿单;拿单生撒拔;
Atayi anali abambo ake a Natani, Natani anali abambo ake a Zabadi,
37 撒拔生以弗拉;以弗拉生俄备得;
Zabadi anali abambo a Efilali, Efilali anali abambo a Obedi,
38 俄备得生耶户;耶户生亚撒利雅;
Obedi anali abambo a Yehu, Yehu anali abambo a Azariya,
39 亚撒利雅生希利斯;希利斯生以利亚萨;
Azariya anali abambo a Helezi, Helezi anali abambo a Eleasa,
40 以利亚萨生西斯买;西斯买生沙龙;
Eleasa anali abambo ake a Sisimai, Sisimai anali abambo a Salumu,
41 沙龙生耶加米雅;耶加米雅生以利沙玛。
Salumu anali abambo a Yekamiya, Yekamiya anali abambo a Elisama.
42 耶拉篾兄弟迦勒的长子米沙,是西弗之祖玛利沙的儿子,是希伯 之祖。
Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa: Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.
43 希伯 的儿子是可拉、他普亚、利肯、示玛。
Ana a Hebroni anali awa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
44 示玛生拉含,是约干之祖。利肯生沙买。
Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai.
45 沙买的儿子是玛云;玛云是伯·夙之祖。
Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.
46 迦勒的妾以法生哈兰、摩撒、迦谢;哈兰生迦卸。(
Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.
47 雅代的儿子是利健、约坦、基珊、毗力、以法、沙亚弗。)
Ana a Yahidai anali awa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.
48 迦勒的妾玛迦生示别、特哈拿,
Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana.
49 又生麦玛拿之祖沙亚弗、抹比拿和基比亚之祖示法。迦勒的女儿是押撒。
Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa.
50 迦勒的子孙就是以法她的长子、户珥的儿子,记在下面:基列·耶琳之祖朔巴,
Izi zinali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa: Sobala abambo a Kiriati Yearimu,
51 伯利恒之祖萨玛,伯迦得之祖哈勒。
Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.
52 基列·耶琳之祖朔巴的子孙是哈罗以和一半米努·哈人。
Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi: Harowe, theka la banja la Manahati,
53 基列·耶琳的诸族是以帖人、布特人、舒玛人、密来人,又从这些族中生出琐拉人和以实陶人来。
ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.
54 萨玛的子孙是伯利恒人、尼陀法人、亚他绿·伯·约押人、一半玛拿哈人、琐利人,
Zidzukulu za Salima zinali izi: Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori,
55 和住雅比斯众文士家的特拉人、示米押人、苏甲人。这都是基尼人利甲家之祖哈末所生的。
ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.

< 历代志上 2 >