< Zefaniya 1 >

1 Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda. 2 “Ndidzawononga kotheratu zinthu zonse pa dziko lapansi,” akutero Yehova. 3 “Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe; ndidzawononga mbalame zamlengalenga ndi nsomba za mʼnyanja. Ndidzawononga anthu oyipa, ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,” akutero Yehova. 4 Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala, mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano: 5 amene amagwada pa madenga a nyumba zawo kupembedza zolengedwa zamumlengalenga, amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova, komanso mʼdzina la Moleki, 6 amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova, osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova. 7 Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova, chifukwa tsiku la Yehova layandikira. Yehova wakonzekera kupereka nsembe; wapatula iwo amene wawayitana. 8 Pa tsiku la nsembe ya Yehova ndidzalanga akalonga ndi ana aamuna a mfumu ndi onse amene amavala zovala zachilendo. 9 Pa tsiku limenelo ndidzalanga onse amene safuna kuponda pa chiwundo, amene amadzaza nyumba ya ambuye awo ndi chiwawa ndi chinyengo. 10 “Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova, “Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba, kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano, ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri. 11 Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika; a malonda anu onse adzapululidwa, ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa. 12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale ndi kulanga onse amene sakulabadira, amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa, amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse, chabwino kaya choyipa.’ 13 Chuma chawo chidzafunkhidwa, nyumba zawo zidzagwetsedwa. Adzamanga nyumba, koma osakhalamo; adzadzala minda ya mpesa koma sadzamwako vinyo wake.” 14 Tsiku lalikulu la Yehova layandikira, layandikira ndipo lifika msanga. Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa, ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri. 15 Tsiku limenelo lidzakhala la ukali, tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni, tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko, tsiku la mdima ndi lachisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani. 16 Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo, tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa ndi nsanja za pa ngodya. 17 Ndidzabweretsa msautso pa anthu ndipo adzayenda ngati anthu osaona, chifukwa achimwira Yehova, magazi awo adzamwazika ngati fumbi ndi mnofu wawo ngati ndowe. 18 Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Dziko lonse lapansi lidzanyeka mʼmoto wa nsanje yake chifukwa adzakantha modzidzimutsa onse okhala pa dziko lapansi.

< Zefaniya 1 >