< Zekariya 13 >

1 “Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.
In that day there shall be a fountain opened to the house of David and to the inhabitants of Jerusalem, for sin and for uncleanness.
2 “Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa.
And it shall come to pass in that day, says Jehovah of hosts, that I will cut off the names of the idols out of the land, and they shall no more be remembered. And I will also cause the prophets and the unclean spirit to pass out of the land.
3 Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.
And it shall come to pass that, when any shall yet prophesy, then his father and his mother who begot him shall say to him, Thou shall not live, for thou speak lies in the name of Jehovah. And his father and his mother who begot him shall thrust him through when he prophesies.
4 “Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.
And it shall come to pass in that day, that the prophets shall be ashamed each one of his vision, when he prophesies, nor shall they wear a hairy mantle to deceive.
5 Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’
But he shall say, I am no prophet. I am a tiller of the ground, for I have been made a bondman from my youth.
6 Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’
And a man shall say to him, What are these wounds between thine arms? Then he shall answer, Those with which I was wounded in the house of my friends.
7 “Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga, ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Kantha mʼbusa ndipo nkhosa zidzabalalika, ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.
Awake, O sword, against my shepherd, and against the man who is my companion, says Jehovah of hosts. Smite the shepherd, and the sheep shall be scattered. And I will turn my hand upon the little ones.
8 Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse, “zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka; koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.
And it shall come to pass, that in all the land, says Jehovah, two parts therein shall be cut off and die, but the third shall be left in it.
9 Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto; ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide. Adzayitana pa dzina langa ndipo Ine ndidzawayankha; Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’”
And I will bring the third part into the fire, and will refine them as silver is refined, and will try them as gold is tried. They shall call on my name, and I will hear them. I will say, It is my people, and they shall say, Jehovah is my God.

< Zekariya 13 >