< Nyimbo ya Solomoni 3 >

1 Usiku wonse ndili pa bedi langa ndinafunafuna amene mtima wanga umamukonda; ndinamufunafuna koma osamupeza. 2 Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda, mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake; ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda. Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza. 3 Alonda anandipeza pamene ankayendera mzinda. “Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?” 4 Nditawapitirira pangʼono ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda. Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, mʼchipinda cha amene anandibereka. 5 Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. 6 Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu ngati utsi watolotolo, wonunkhira mure ndi lubani, zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda? 7 Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni, choperekezedwa ndi asilikali 60, anthu amphamvu a ku Israeli, 8 onse atanyamula lupanga, onse odziwa bwino nkhondo, aliyense ali ndi lupanga pambali pake, kukonzekera zoopsa za usiku. 9 Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi; anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni. 10 Milongoti yake anayipanga yasiliva, kumbuyo kwake kwa golide. Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo, anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondi cha akazi a ku Yerusalemu. 11 Tukulani inu akazi a ku Ziyoni ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu, chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unasangalala.

< Nyimbo ya Solomoni 3 >