< Masalimo 1 >

1 Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza. 2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku. 3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho. 4 Sizitero ndi anthu oyipa! Iwo ali ngati mungu umene umawuluzidwa ndi mphepo. 5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo, kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama. 6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama, koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.

< Masalimo 1 >