< Masalimo 97 >

1 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere. 2 Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu. 3 Moto umapita patsogolo pake ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse. 4 Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera. 5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi. 6 Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake. 7 Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse! 8 Ziyoni akumva ndipo akukondwera, midzi ya Yuda ikusangalala chifukwa cha maweruzo anu Yehova. 9 Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse. 10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa 11 Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima. 12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera.

< Masalimo 97 >