< Masalimo 97 >

1 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere.
The LORD reigns. Let the earth rejoice. Let the multitude of islands be glad.
2 Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
Clouds and darkness are around him. Righteousness and justice are the foundation of his throne.
3 Moto umapita patsogolo pake ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
A fire goes before him, and burns up his adversaries on every side.
4 Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
His lightning lights up the world. The earth sees, and trembles.
5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
The mountains melt like wax at the presence of the LORD, at the presence of the Lord of the whole earth.
6 Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.
The heavens declare his righteousness. All the peoples have seen his glory.
7 Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse!
Let all them be shamed who serve engraved images, who boast in their idols. Worship him, all you gods.
8 Ziyoni akumva ndipo akukondwera, midzi ya Yuda ikusangalala chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
Zion heard and was glad. The daughters of Judah rejoiced, because of your judgments, LORD.
9 Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.
For you, LORD, are most high above all the earth. You are exalted far above all gods.
10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
You who love the LORD, hate evil. He preserves the souls of his faithful ones. He delivers them out of the hand of the wicked.
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
Light is sown for the righteous, and gladness for the upright in heart.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera.
Be glad in the LORD, you righteous people. Give thanks to his holy Name.

< Masalimo 97 >