< Masalimo 95 >

1 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe, tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu 2 Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo. 3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu, mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse. 4 Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi, ndipo msonga za mapiri ndi zake. 5 Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye, ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma. 6 Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu; 7 pakuti Iye ndiye Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za mʼdzanja lake. Lero ngati inu mumva mawu ake, 8 musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu. 9 Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa, ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita. 10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo; ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera ndipo sanadziwe njira zanga.” 11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti, “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”

< Masalimo 95 >