< Masalimo 93 >

1 Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe. 2 Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; Inu ndinu wamuyaya. 3 Nyanja zakweza Inu Yehova, nyanja zakweza mawu ake; nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo. 4 Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri, ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja, Yehova mmwamba ndi wamphamvu. 5 Malamulo anu Yehova ndi osasinthika; chiyero chimakongoletsa nyumba yanu mpaka muyaya.

< Masalimo 93 >