< Masalimo 86 >

1 Pemphero la Davide. Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
A prayer of David. Listen, Yahweh, and answer me, for I am poor and oppressed.
2 Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu. Inu ndinu Mulungu wanga; pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga.
Protect me, for I am loyal; my God, save your servant who trusts in you.
3 Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
Be merciful to me, Lord, for I cry out to you all day long.
4 Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye, pakuti ndimadalira Inu.
Make your servant glad, for to you, Lord, I lift up my soul.
5 Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino, wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
You, Lord, are good, and ready to forgive, and you show great mercy to all those who cry out to you.
6 Yehova imvani pemphero langa; mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
Yahweh, listen to my prayer; hear the sound of my pleas.
7 Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha.
In the day of my trouble I call on you, for you will answer me.
8 Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye; palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
There is no one who compares to you among the gods, Lord. There are no deeds like your deeds.
9 Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye; iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
All the nations that you have made will come and bow before you, Lord. They will honor your name.
10 Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.
For you are great and do wonderful things; you only are God.
11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova, ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu; patseni mtima wosagawikana kuti ndilemekeze dzina lanu.
Teach me your ways, Yahweh. Then I will walk in your truth. Unite my heart to reverence you.
12 Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
Lord my God, I will praise you with my whole heart; I will glorify your name forever.
13 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine; mwandipulumutsa ku malo ozama a manda. (Sheol h7585)
For great is your covenant faithfulness toward me; you have rescued my life from the depths of Sheol. (Sheol h7585)
14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufuna kundipha, amene salabadira za Inu.
God, the arrogant have risen up against me. A gang of violent men seek my life. They have no regard for you.
15 Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
But you, Lord, are a merciful and gracious God, slow to anger, and abundant in covenant faithfulness and trustworthiness.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo; perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
Turn toward me and have mercy on me; give your strength to your servant; save the son of your servant woman.
17 Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi, pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.
Show me a sign of your favor. Then those who hate me will see it and be put to shame because you, Yahweh, have helped me and comforted me.

< Masalimo 86 >