< Masalimo 70 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho. Fulumirani Mulungu kundipulumutsa; Yehova bwerani msanga kudzandithandiza. 2 Iwo amene akufunafuna moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene akukhumba chiwonongeko changa abwezedwe mopanda ulemu. 3 Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,” abwerere chifukwa cha manyazi awo. 4 Koma onse amene akufunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!” 5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa; bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu. Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga; Inu Yehova musachedwe.

< Masalimo 70 >