< Masalimo 66 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo. Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi! 2 Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero. 3 Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu. 4 Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” (Sela) 5 Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu. 6 Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye. 7 Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule. 8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke; 9 Iye watchinjiriza miyoyo yathu ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke. 10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva. 11 Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu. 12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu; ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi, koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka. 13 Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga. 14 Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto. 15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. (Sela) 16 Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira. 17 Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga. 18 Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera; 19 koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga. 20 Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine!

< Masalimo 66 >