< Masalimo 62 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide. Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha; chipulumutso changa chimachokera kwa Iye. 2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka. 3 Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti? Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba, ngati mpanda wogwedezeka? 4 Iwo akufunitsitsa kumugwetsa kuti achoke pa malo ake apamwamba. Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza. Ndi pakamwa pawo amadalitsa koma mʼmitima yawo amatemberera. 5 Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga; chiyembekezo changa chichokera mwa Iye. 6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka. 7 Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu: Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga. 8 Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. (Sela) 9 Anthu wamba ndi mpweya chabe; anthu apamwamba ndi bodza chabe; ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe; iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe 10 Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho. 11 Mulungu wayankhula kamodzi, ine ndamvapo zinthu ziwiri; choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu, 12 komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika. Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu molingana ndi ntchito zake.

< Masalimo 62 >