< Masalimo 61 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe. Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu; mvetserani pemphero langa. 2 Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka; tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo. 3 Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga, nsanja yolimba polimbana ndi adani anga. 4 Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu. 5 Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga; mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu. 6 Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu, zaka zake kwa mibado yochuluka. 7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya; ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze. 8 Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

< Masalimo 61 >